Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

external-link copy
142 : 7

۞ وَوَٰعَدۡنَا مُوسَىٰ ثَلَٰثِينَ لَيۡلَةٗ وَأَتۡمَمۡنَٰهَا بِعَشۡرٖ فَتَمَّ مِيقَٰتُ رَبِّهِۦٓ أَرۡبَعِينَ لَيۡلَةٗۚ وَقَالَ مُوسَىٰ لِأَخِيهِ هَٰرُونَ ٱخۡلُفۡنِي فِي قَوۡمِي وَأَصۡلِحۡ وَلَا تَتَّبِعۡ سَبِيلَ ٱلۡمُفۡسِدِينَ

Ndipo tidamlonjeza Mûsa masiku makumi atatu (kuti achite mapemphero kuti kenako timpatse Taurat). Ndipo tidawakwaniritsa ndi masiku khumi; chomwecho lidakwanira pangano la Mbuye wake (lopita kukampatsa Tauratiyo) m’masiku makumi anayi. Ndipo Mûsa adati kwa m’bale wake Harun: “Lowa m’malo mwanga pa (kuwatsogolera) anthu angawa. Ndipo konza; usatsate njira ya oononga.” info
التفاسير: