[183] Aliyense adzapeza chilango chachikulu. Ndipo awo amene adasokeretsedwa: (a) Adzapeza chilango chifukwa cholola kusokeretsedwa pomwe adapatsidwa nzeru zowazindikiritsa zabwino ndi zoipa. (b) Adzapeza chilango chifukwa chochita machimowo. Tsono amene adali kusokeretsa anzawo:
a) Adzapeza chilango chifukwa chakuchita kwawo machimo.
b) Adzapeza chilango chifukwa chakuwasokeretsa anthu omwe adawasokeretsa.
c) Adzapeza chilango chifukwa chakuyambitsa machimowo.
d) Adzapeza chilango chifukwa chowasiira anzawo odza m’mbuyo mwawo machimo powatsanzira iwo.