[353] Ayah imeneyi ikulongosola nkhani ya kusamutsidwa kwa Ayuda otchedwa Bani Nadhir mu mzinda wa Madina. Ayuda adasamutsidwa mu mzinda wa Madina chifukwa cha kuswa mapangano okhalirana mwa mtendere ndi Asilamu.
[354] (Ndime 5-7) Ndime zimenezi zikufotokoza za kagawidwe ka chuma chosiyidwa ndi adani pankhondo. Chumacho sichongogawira amene amachita nkhondo okha ayi. Kapena kugawana akulu-akulu okha monga momwe amachitira ena omwe sali Asilamu pa nkhondo zawo. Chifukwa kutero ndiye kuti chumacho chizingozungulira pakati pa anthu olemera okhaokha. Chisilamu chikulamula kuti chuma choterechi chigawidwe kwa onse kuti umphawi uwachokere onse.