[288] Kutsutsana pa zinthu za chipembedzo popanda kudziwa ndi kukhala ndi umboni wokwanira nkoletsedwa zedi. Maphunziro enieni amene angamzindikiritse munthu za chipembedzo, ndi omwe akupezeka m’Qur’an ndi m’mahadisi a Mtumiki (s.a.w) omwe ali owona, ndi maphunziro amene akupezeka m’mabuku ophunzitsa malamulo achipembedzo omwe ali ovomerezeka ndi atsogoleri a Chisilamu, osati buku lililonse lolembedwa ndi munthu wamba.
[289] Allah watibweretsa pano padziko lapansi kuti tiyesedwe mayeso akulungama ndi kusalungama tsiku lachimaliziro lisanadze. Choncho tipirire ndi kugwiritsa zimene Allah ndi Mtumiki Wake atiuza. Tidziwe kuti pali mavuto pali zabwino.