[254] M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.