Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala

Hûd

external-link copy
1 : 11

الٓرۚ كِتَٰبٌ أُحۡكِمَتۡ ءَايَٰتُهُۥ ثُمَّ فُصِّلَتۡ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ خَبِيرٍ

Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 11

أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۚ إِنَّنِي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ وَبَشِيرٞ

(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 11

وَأَنِ ٱسۡتَغۡفِرُواْ رَبَّكُمۡ ثُمَّ تُوبُوٓاْ إِلَيۡهِ يُمَتِّعۡكُم مَّتَٰعًا حَسَنًا إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى وَيُؤۡتِ كُلَّ ذِي فَضۡلٖ فَضۡلَهُۥۖ وَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٖ كَبِيرٍ

Ndikuti mupemphe chikhululuko kwa Mbuye wanu ndipo mulape kwa Iye. Akupatsani chisangalalo chabwino mpakana m’nthawi yoikidwa. Ndipo adzampatsa (tsiku lachimaliziro) aliyense wochita zabwino ubwino wake. Koma, ngati mupotoka ine kwanga nkukuoperani za chilango cha tsiku lalikulu. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 11

إِلَى ٱللَّهِ مَرۡجِعُكُمۡۖ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ

Kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 11

أَلَآ إِنَّهُمۡ يَثۡنُونَ صُدُورَهُمۡ لِيَسۡتَخۡفُواْ مِنۡهُۚ أَلَا حِينَ يَسۡتَغۡشُونَ ثِيَابَهُمۡ يَعۡلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعۡلِنُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Tamverani! Iwo akubisa zimene zili m’mitima yawo kuti amubise Iye (Allah). Mverani! Ndithudi pamene akuzifunda nsalu zawo Iye akudziwa zimene akuzibisa ndi zimene akuzionetsa. Ndithudi Iye ndiwodziwa za mzifuwa. info
التفاسير: