Übersetzung der Bedeutungen von dem heiligen Quran - Die Übersetzung in Chichewa - Khalid Ibrahim Bityala.

Nummer der Seite:close

external-link copy
89 : 27

مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ خَيۡرٞ مِّنۡهَا وَهُم مِّن فَزَعٖ يَوۡمَئِذٍ ءَامِنُونَ

Amene adzadza ndi chabwino, adzalandira mphoto yoposa chabwinocho; ndikuopsa kwa tsiku limenelo, iwo adzakhala nako mwamtendere. info
التفاسير:

external-link copy
90 : 27

وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَكُبَّتۡ وُجُوهُهُمۡ فِي ٱلنَّارِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

Koma amene adzadza ndi choipa, adzaponyedwa ku Moto champhumi (ndipo kudzanenedwa kwa iwo): “Kodi mungalipidwe (zina) osati zomwe mumachita?” info
التفاسير:

external-link copy
91 : 27

إِنَّمَآ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ رَبَّ هَٰذِهِ ٱلۡبَلۡدَةِ ٱلَّذِي حَرَّمَهَا وَلَهُۥ كُلُّ شَيۡءٖۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ

(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu ndalamulidwa kumpembedza Mbuye wa mzinda uwu, Yemwe adaukhazika wopatulika. Ndipo zinthu zonse nza Iye (Allah), ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa ogonjera (Allah).” info
التفاسير:

external-link copy
92 : 27

وَأَنۡ أَتۡلُوَاْ ٱلۡقُرۡءَانَۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَقُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُنذِرِينَ

“Ndiponso (ndalamulidwa) kuti ndiwerenge Qur’an.” Ndipo amene waongoka, ubwino wa kuongokako uli pa iye; ndipo amene wasokera, (wadzisokeretsa yekha). Nena: “Ndithu ine sikanthu koma ndine mmodzi wa achenjezi. (Ndilibe udindo wina woposa uwu).” info
التفاسير:

external-link copy
93 : 27

وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ سَيُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ فَتَعۡرِفُونَهَاۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ

Ndipo nena: “Kuyamikidwa konse (kwabwino) nkwa Allah; posachedwapa akusonyezani zizindikiro Zake, ndipo muzizindikira.” Ndipo Mbuye wako sali woiwala zimene mukuchita. info
التفاسير: