[30] Otsatira Mneneri (maswahaba) anakumana ndi osakhulupilira padeti ya 30, m’mwezi wa 6 pakalendala ya Chisilamu. Ena amaganiza kuti detilo la pa 30 lidali la m’mwezi wa Rajabu omwe ngoletsedwa kuchitamo nkhondo. Tero Aquraish adamnamizira Muhammad (s.a.w) kuti waswa ulemelero wa miyezi yopatulika. Ndipo adabwera kukamfunsa kuti: “Kodi ndimmene ukuchitira?” Umo ndi momwe Allah adawayankhira.
[31] Apa akufotokoza kuti masautso ndi mavuto omwe mowa ndi njuga zimadzetsa ngaakulu zedi kuposa ubwino wake. Mowa umamchotsa munthu nzeru pomwe nzeru ndidalitso lalikulu kuposa chilichonse. Ndipo mowa umamuonongera munthu chuma ndi kumdzetsera matenda m’thupi mwake. Nayonso njuga nchimodzimodzi. Imawononga chuma ndi kuyambitsa chidani pakati pa anthu. Zonsezi zimadzetsa chisokonezo ku mtundu wa munthu.