[494] Ili ndi lonjezo la Allah kwa Mneneri wake (Muhammad) (s.a.w) kuti amthandiza kumpulumutsa kwa adani ake amene adali kumuzunza ndi kufuna kumupha. Lonjezoli lidali lakuti iye adzaulamulira mzinda wa adaniwo momwe adamutulutsa.
[495] Mneneri (s.a.w) pamene adalowa mu mzinda wa Makka ndi kugonjetsa adani ake monga momwe Allah adamulonjezera, a kafiri adali kubwera m’mafukomafuko kudzalowa m’chipembedzo cha Chisilamu.
[496] Tanthauzo la kuuzidwa Mneneri Muhammad (s.a.w) kuti zikachitika zimene adalonjezedwa, amulemekeze Mbuye wake, amupemphe chikhululuko, chikhalirecho iye adali kuchita zimenezo, izi zimatanthauza kuti moyo wake wayandikira kutha, watsala pang’ono kumwalira. Choncho adalamulidwa kuonjezera mapemphero kuti aonjezere kulinganiza tsiku lake lomaliza. Imeneyi ndi imodzi mwa Surah zimene zidavumbulutsidwa kotsirizira kwa moyo wa Mtumiki (s.a.w). Pamene idavumbulutsidwa Surayi, ena mwa maswahaba (omutsatira) adazindikira chinsinsi cha Surayi; adali kulira poona kuti Mneneri (s.a.w) amwalira posachedwa. Pambuyo povumbulutsidwa Surayi, Mneneri (s.a.w) sadakhale moyo nthawi yaitali.