Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice:close

external-link copy
49 : 34

قُلۡ جَآءَ ٱلۡحَقُّ وَمَا يُبۡدِئُ ٱلۡبَٰطِلُ وَمَا يُعِيدُ

Nena: “Choonadi chadza (chisilamu); ndipo chabodza (chipembedzo cha mafano) sichidzetsa zachilendo, ndiponso sichibwerera (kukhala ndi nyonga monga kale).” info
التفاسير:

external-link copy
50 : 34

قُلۡ إِن ضَلَلۡتُ فَإِنَّمَآ أَضِلُّ عَلَىٰ نَفۡسِيۖ وَإِنِ ٱهۡتَدَيۡتُ فَبِمَا يُوحِيٓ إِلَيَّ رَبِّيٓۚ إِنَّهُۥ سَمِيعٞ قَرِيبٞ

Nena: “Ngati ndasokera, ndiye kuti ndadzisokeretsa ndekha (ndadziyika ndekha m’mavuto). Koma ngati ndaongoka, ndichifukwa cha zimene akundivumbulutsira Mbuye wanga. Ndithu Iye Ngwakumva; ali pafupi (ndi aliyense).” info
التفاسير:

external-link copy
51 : 34

وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذۡ فَزِعُواْ فَلَا فَوۡتَ وَأُخِذُواْ مِن مَّكَانٖ قَرِيبٖ

Ndipo ukadaona pamene adzanjenjemera (akadzachiona chilango cha Allah, adzayesera kuthawa), koma sipadzapezeka pothawira, ndipo adzagwidwa pamtunda wapafupi (asanafike kutali). info
التفاسير:

external-link copy
52 : 34

وَقَالُوٓاْ ءَامَنَّا بِهِۦ وَأَنَّىٰ لَهُمُ ٱلتَّنَاوُشُ مِن مَّكَانِۭ بَعِيدٖ

Ndipo adzanena (mophuphaphupha): “Tachikhulupirira (tsopano chipembedzo cha Chisilamu).” Koma iwo angaulandire chotani (Usilamu) kumeneko (komwe) ndikumalo akutali. info
التفاسير:

external-link copy
53 : 34

وَقَدۡ كَفَرُواْ بِهِۦ مِن قَبۡلُۖ وَيَقۡذِفُونَ بِٱلۡغَيۡبِ مِن مَّكَانِۭ بَعِيدٖ

Pomwe chikhalirenicho adachikana kale (Chisilamu). Ndipo chobisika ankachigenda (ndi bodza) kuchokera kumalo akutali. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 34

وَحِيلَ بَيۡنَهُمۡ وَبَيۡنَ مَا يَشۡتَهُونَ كَمَا فُعِلَ بِأَشۡيَاعِهِم مِّن قَبۡلُۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ فِي شَكّٖ مُّرِيبِۭ

Ndipo padzatsekeka pakati pawo ndi zimene akuzilakalaka, monga momwe adachitidwira anzawo akale. Ndithu iwo adali m’chikaiko chowakaikitsa (uthenga wa Allah). info
التفاسير: