[320] Imamu Ibnu Jarir Taburiyu adalemba m’buku lake kuti Anasi Bun Malik adati:- M’bale wa bambo anga, Anasi bun Nadhari sadakhale nawo pa nkhondo ya Badri, ndipo adati: “Sindidakhale pamodzi ndi Mtumiki pa nkhondo yoyamba. Ngati Allah atandifikitsa pa nkhondo ina Allah adzaona zimene ndidzachita pomenya nkhondo modzipereka.” Pa tsiku la nkhondo ya Uhud, pamene Asilamu adabalalikana kuthawa ndipo iye adati:- “E Allah! Ine ndikudzipatula ku zomwe achita awa, osakhulupilira. Ndiponso ndikudandaula mzimene achita awa, Asilamu amene athawa.” Kenako adayenda ndi lupanga lake nakumana ndi Saad bun Muadhi, nati: “E iwe Saad! Ine ndikumva fungo la ku Munda wa mtendere pafupi ndi phiri ili la Uhud.” Kenako adachita nkhondo kufikira adaphedwa. Ndipo Saad adati: “E iwe Mtumiki wa Allah! Sindinathe kuchita chimene iye adachita.” Anasi bun Malik adati: “Tidampeza ali m’gulu lophedwa uku ali ndi mabala okwanira 80, ena otemedwa ndi malupanga, ndipo ena olasidwa ndi mikondo ndi mipaliro. Sitidamzindikire kufikira pamene adadza mlongo wake naamzindikira kupyolera m’nsonga za zala zake.” Ndipo Anasi adatinso: “Tidali kukambirana kuti ndime iyi ikukamba za iye.”
[321] Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupilira (akafiri) a Chiarabu ochokera mu mtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi mapangano ndi Mtumiki (s.a.w) okhalirana mwa mtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (s.a.w) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, pomwe ena adawagwira monga akaidi a pankhondo.
[322] Mu Ayah imeneyi, akazi a Mtumiki (s.a.w) akuuzidwa kuti iwo akachimwa, Allah adzawalanga chilango chachikulu kuposa momwe akadalangidwira akazi ena omwe sali akazi a Mtumiki (s.a.w). Izi nchifukwa chakuti, iwo ndi atsogoleri; chilichonse chomwe iwo achita, choipa kapena chabwino, chidzatsatidwa ndi ena. Akachita chabwino, Allah adzawapatsa malipiro aakulu. Ndipo akachita choipa, adzawalanga ndi chilango chachikulu. Choncho aliyense amene ndi mtsogoleri, aonetsetse kuti akuchita zolungama zokhazokha.