Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala

Broj stranice: 356:350 close

external-link copy
54 : 24

قُلۡ أَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَۖ فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَإِنَّمَا عَلَيۡهِ مَا حُمِّلَ وَعَلَيۡكُم مَّا حُمِّلۡتُمۡۖ وَإِن تُطِيعُوهُ تَهۡتَدُواْۚ وَمَا عَلَى ٱلرَّسُولِ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ

Nena: “Mverani Allah, ndiponso Mverani Mtumiki. Koma ngati mutembenuka, iye ali nazo zimene wasenzetsedwa (kuti azifikitse kwa inu), (ndipo) inunso muli nazo zimene mwasenzetsedwa (kuti muzitsate). Ndipo mukamumvera, muongoka. Ndipo pa Mtumiki palibe china chake koma kufikitsa (uthenga) momveka. info
التفاسير:

external-link copy
55 : 24

وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ مِنكُمۡ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَيَسۡتَخۡلِفَنَّهُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ كَمَا ٱسۡتَخۡلَفَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ وَلَيُمَكِّنَنَّ لَهُمۡ دِينَهُمُ ٱلَّذِي ٱرۡتَضَىٰ لَهُمۡ وَلَيُبَدِّلَنَّهُم مِّنۢ بَعۡدِ خَوۡفِهِمۡ أَمۡنٗاۚ يَعۡبُدُونَنِي لَا يُشۡرِكُونَ بِي شَيۡـٔٗاۚ وَمَن كَفَرَ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ

Allah walonjeza mwa inu amene akhulupirira ndikuchita ntchito yabwino kuti ndithu awathandiza kukhala oyang’anira pa dziko monga momwe adawachitira amene adalipo kale kukhala oyang’anira; ndipo ndithu awalimbikitsira chipembedzo chawo chimene wawayanja nacho; ndipo awachotsera mantha awo kukhala opanda mantha.” Akhale akundilambira Ine, osandiphatikiza ndi chilichonse. Ndipo amene asiye kukhulupirira pambuyo pa zimenezi, iwo ngakuswa malamulo. info
التفاسير:

external-link copy
56 : 24

وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Choncho, pempherani Swala moyenera ndi kupereka “Zakaat;” ndiponso mverani Mtumiki kuti muchitiridwe chisoni. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 24

لَا تَحۡسَبَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِۚ وَمَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُۖ وَلَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ

Amene sadakhulupirire musawaganizire kuti angamulepheretse Allah pa dziko (kuwalanga), ndipo malo awo ndi ku Moto. Ha! Ayipirenji malo obwererako! info
التفاسير:

external-link copy
58 : 24

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِيَسۡتَـٔۡذِنكُمُ ٱلَّذِينَ مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡ وَٱلَّذِينَ لَمۡ يَبۡلُغُواْ ٱلۡحُلُمَ مِنكُمۡ ثَلَٰثَ مَرَّٰتٖۚ مِّن قَبۡلِ صَلَوٰةِ ٱلۡفَجۡرِ وَحِينَ تَضَعُونَ ثِيَابَكُم مِّنَ ٱلظَّهِيرَةِ وَمِنۢ بَعۡدِ صَلَوٰةِ ٱلۡعِشَآءِۚ ثَلَٰثُ عَوۡرَٰتٖ لَّكُمۡۚ لَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ وَلَا عَلَيۡهِمۡ جُنَاحُۢ بَعۡدَهُنَّۚ طَوَّٰفُونَ عَلَيۡكُم بَعۡضُكُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ

E inu amene mwakhulupirira! Akuodireni amene manja anu akumanja apeza ndi amene mwa inu sanathe nsinkhu, awodire nthawi zitatu: Isanapempheredwe Swala ya m’mawa, ndi pamene mukuvula nsalu zanu nthawi yamasana (kuti mupumule), ndi pambuyo pa Swala ya Isha (usiku). Izi ndi nthawi zitatu zomwe inu mumakhala wamba. Palibe uchimo pa inu ngakhale pa iwo pambuyo pa nthawi zimenezo (kulowa popanda kuodira); mumazungulirana pakati panu, umo ndi momwe akukufotokozerani Allah Ayah (ndime) Zake. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير: