আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

পৃষ্ঠা নং:close

external-link copy
20 : 47

وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَوۡلَا نُزِّلَتۡ سُورَةٞۖ فَإِذَآ أُنزِلَتۡ سُورَةٞ مُّحۡكَمَةٞ وَذُكِرَ فِيهَا ٱلۡقِتَالُ رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ نَظَرَ ٱلۡمَغۡشِيِّ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡمَوۡتِۖ فَأَوۡلَىٰ لَهُمۡ

Ndipo amene akhulupirira akunena (chifukwa cha mazunzo omwe amawapeza kuchokera kwa osakhulupirira kuti) kodi nchifukwa ninji siikuvumbulutsidwa sura (yotiloleza kumenyana ndi osakhulupirira Allah amene akutiputa)? Koma ikavumbulutsidwa Sura yokhazikika (lamulo lake), ndipo mkati mwake ndi kutchulidwa nkhani zankhondo, uwaona amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akukuyang’ana m’mayang’anidwe a yemwe akukomoka ndi imfa, (chifukwa cha kulida lamulo lomenyana ndi osakhulupirira), basi kuonongeka ndi kwawo. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 47

طَاعَةٞ وَقَوۡلٞ مَّعۡرُوفٞۚ فَإِذَا عَزَمَ ٱلۡأَمۡرُ فَلَوۡ صَدَقُواْ ٱللَّهَ لَكَانَ خَيۡرٗا لَّهُمۡ

(Zofunika ndi) kumvera ndi mawu abwino ndi kuti chinthu chikatsimikizika (achichite). Ngati akadamumvera Allah, ndithu zikadakhala zabwino kwa iwo. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 47

فَهَلۡ عَسَيۡتُمۡ إِن تَوَلَّيۡتُمۡ أَن تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَتُقَطِّعُوٓاْ أَرۡحَامَكُمۡ

Mwina mwake inu mukanyoza (Chisilamu), mubwerera m’mbuyo ku zomwe mudali nazo (m’nthawi ya umbuli) monga kuononga pa dziko ndi machimo) ndi kudula chibale chanu. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 47

أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَعَنَهُمُ ٱللَّهُ فَأَصَمَّهُمۡ وَأَعۡمَىٰٓ أَبۡصَٰرَهُمۡ

Oterewo ndiamene Allah wawatembelera ndi kuwagonthetsa ndi kuwachititsa khungu maso awo. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 47

أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ ٱلۡقُرۡءَانَ أَمۡ عَلَىٰ قُلُوبٍ أَقۡفَالُهَآ

Kodi sakuilingalira Qur’an? Kapena m’mitima mwawo m’motsekedwa ndi akabali (maloko) ake? info
التفاسير:

external-link copy
25 : 47

إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱرۡتَدُّواْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ ٱلۡهُدَى ٱلشَّيۡطَٰنُ سَوَّلَ لَهُمۡ وَأَمۡلَىٰ لَهُمۡ

Ndithu amene akubwerera m’mbuyo (kusiya chipembedzo chawo nkubwerera ku zosakhulupirira Allah) chiongoko chitawaonekera poyera satana ndiamene wawanyenga, ndipo Allah akuwapatsa nthawi. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 47

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُواْ لِلَّذِينَ كَرِهُواْ مَا نَزَّلَ ٱللَّهُ سَنُطِيعُكُمۡ فِي بَعۡضِ ٱلۡأَمۡرِۖ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ إِسۡرَارَهُمۡ

Zimenezo nkaamba kakuti iwo adanena kwa omwe amada zimene Allah wavumbulutsa (kuti): “Tidzakumverani m’zinthu zina (zimene mukutsutsana ndi Mtumiki{s.a.w}).” Ndipo Allah akudziwa zobisika zawo. info
التفاسير:

external-link copy
27 : 47

فَكَيۡفَ إِذَا تَوَفَّتۡهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَضۡرِبُونَ وُجُوهَهُمۡ وَأَدۡبَٰرَهُمۡ

Kodi adzakhala bwanji pamene angelo azidzatenga mizimu yawo uku akumenya nkhope zawo ndi misana yawo? info
التفاسير:

external-link copy
28 : 47

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمُ ٱتَّبَعُواْ مَآ أَسۡخَطَ ٱللَّهَ وَكَرِهُواْ رِضۡوَٰنَهُۥ فَأَحۡبَطَ أَعۡمَٰلَهُمۡ

Zimenezi (imfa yoopsayi) nkaamba kakuti iwo adatsata zomwe zidakwiitsa Allah ndi kuda zomusangalatsa (Allah); choncho adaziwononga zochita zawo. info
التفاسير:

external-link copy
29 : 47

أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ أَن لَّن يُخۡرِجَ ٱللَّهُ أَضۡغَٰنَهُمۡ

Kodi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akuganiza kuti Allah sangaonetsere poyera kaduka kawo? info
التفاسير: