[252] Omasulira Qur’an akunena kuti ndime iyi idatsika chifukwa cha Ammar Bun Yasir. Opembedza mafano adamgwira ndi kumuvutitsa zedi kufikira iye adawapatsa chomwe iwo ankafuna kwa iye momkakamiza kutero. Anthu adati: “Ndithudi, Ammar watuluka m’Chisilamu.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ndithudi, Ammar ngodzaza ndi chikhulupiliro kuyambira kumutu mpaka kumapazi. Chikhulupiliro chasakanikirana ndi minofu ndi magazi ake.” Zitatero Ammar adabwera kwa Mtumiki (s.a.w) uku akulira. Mtumiki (s.a.w) adati kwa iye: “Kodi ukupeza bwanji mtima wako?” Iye adati: “Ngokhazikika pa chikhulupiliro.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Ngati abwereranso iwenso bwerezanso zimene wanenazo.”