আল-কোৰআনুল কাৰীমৰ অৰ্থানুবাদ - চিচেৱা অনুবাদ- খালিদ ইব্ৰাহীম বেতালা

An-Nahl

external-link copy
1 : 16

أَتَىٰٓ أَمۡرُ ٱللَّهِ فَلَا تَسۡتَعۡجِلُوهُۚ سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 16

يُنَزِّلُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةَ بِٱلرُّوحِ مِنۡ أَمۡرِهِۦ عَلَىٰ مَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦٓ أَنۡ أَنذِرُوٓاْ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱتَّقُونِ

Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.” info
التفاسير:

external-link copy
3 : 16

خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۚ تَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi (osati mwakungoseweretsa chabe) ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazo (ophatikiza Allah ndi mafano). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 16

خَلَقَ ٱلۡإِنسَٰنَ مِن نُّطۡفَةٖ فَإِذَا هُوَ خَصِيمٞ مُّبِينٞ

Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera.[247] info

[247] Apa Allah akunenetsa kuti adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna wopanda pake. Koma munthu pambuyo pokwanira chilengedwe chake akukhala wotsutsana ndi Mlengi wake ndi kumchitira mwano modzitukumula chikhalirecho adalengedwa kuti akhale kapolo wa Allah, osati wopikisana naye.

التفاسير:

external-link copy
5 : 16

وَٱلۡأَنۡعَٰمَ خَلَقَهَاۖ لَكُمۡ فِيهَا دِفۡءٞ وَمَنَٰفِعُ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ

Ndipo adalenga ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi) mwa izo mukupeza zofunda, ndi zothandiza (zina zambiri), ndipo zina mwa izo mumazidya. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 16

وَلَكُمۡ فِيهَا جَمَالٌ حِينَ تُرِيحُونَ وَحِينَ تَسۡرَحُونَ

Ndipo mumakondwa ndi kunyadira chifukwa cha kukongola kwa izo mukamabwera nazo (kuchokera kubusa mimba zitakhuta), ndi popita nazo (kubusa zikuyenda mwandawala). info
التفاسير: