Ndipo tidatsatiza pa mapazi a aneneriwo, Isa (Yesu) mwana wa Mariya kudzatsimikizira zomwe zidali patsogolo pake m’buku la Taurat. Ndipo tidampatsa Injili yomwe m’kati mwake muli chiongoko ndi kuunika; ndikutsimikizira zomwe zidali patsogolo pake za m’buku la Taurat. Ndipo ndi chiongoko ndi ulaliki wabwino kwa oopa (Allah).