[156] Nyama imene aizinga ndi cholinga china, osati ncholinga cha Allah monga:-
(1) Nyama imene aizinga chifukwa chotsirika nyumba kuti ziwanda zisamavutitsemo, kapena nyama imene aizinga pofuna kutsirika mudzi, kapena kuti chaka chino tikapanda kuzinga nyama kubwera matsoka akutiakuti
(2) Nyama imene aizinga pofuna kusangalatsa chiwanda cham’nyumba kapena cham’munda.
(3) Nyama imene aizinga pofuna kutsirika ukwati kuti ulimbe kapena pofuna kutsirika yemwe wabwera kuulendo kuti asamlodze.
(4) Nyama imene aizinga ncholinga choti akataye bwino maliro, ndi kuti mzimu wamalirowo usavutitse anthu pamudzi; nyama zonse zimene zazingidwa ndizolinga monga izi tatchulazi, nzoletsedwa kuzidya. Ndipo kunena koti: “Chimene chafa ndikumenyedwa ncholetsedwa koma pokhapokha mutachipeza chili moyobe nimuchizinga,” tanthauzo lake nkuti nyama imene imadyedwa ngati itafa pazifukwa zina zilizonse, monga kugundidwa ndi galimoto ndi zina zotero ndipo nyamayo sinaferetu kotero kuti nkutheka kuizinga, nyama yotero njololedwa kudya.