E inu amene mwakhulupirira! Musamatsogoze (kulamula chinthu chapachipembedzo kapena cham’dziko) patsogolo pa (mawu a) Allah ndi Mthenga Wake. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.
Ndithu amene akutsitsa mawu awo pamaso pa mtumiki wa Allah, iwo ndiamene Allah wawayeretsa mitima yawo pomuopa Iye; chikhululuko ndi malipiro akulu zidzakhala pa iwo.