[315] M’ndime iyi Allah akutiuza kuti adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi. Komatu nthawi ya masiku amenewa, palibe amene akudziwa tsatanetsatane wake koma Allah Yekha. Choncho tisaganizire kuti masikuwo adali olingana ndi masiku a moyo uno wadziko lapansi.