ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا

رقم الصفحة:close

external-link copy
23 : 3

أَلَمۡ تَرَ إِلَى ٱلَّذِينَ أُوتُواْ نَصِيبٗا مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ يُدۡعَوۡنَ إِلَىٰ كِتَٰبِ ٱللَّهِ لِيَحۡكُمَ بَيۡنَهُمۡ ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٞ مِّنۡهُمۡ وَهُم مُّعۡرِضُونَ

Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza.[63] info

[63] Ndimeyi anthu omasulira Qur’an akuti ikufotokoza nkhani za Ayuda pamene adadza kwa Mtumiki (s.a.w), mmodzi mwa iwo atachita chiwerewere kuti amve chilamulo cha wochita chiwerewere. Mtumiki (s.a.w) anagamula kuti amugende ndi miyala mpaka afe. Koma iwo anakana. Nati: “M’buku lathu mulibe chilamulo chotere.” Ndipo adawauza kuti abwere nalo bukulo. Atabwera nalo anapeza kuti chilamulocho chilimo. Ndipo anawagenda miyala. Zitachitika tero, Ayuda anakwiya.

التفاسير:

external-link copy
24 : 3

ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُواْ لَن تَمَسَّنَا ٱلنَّارُ إِلَّآ أَيَّامٗا مَّعۡدُودَٰتٖۖ وَغَرَّهُمۡ فِي دِينِهِم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ

Zimenezo (kusalabadira malamulo a Allah) nchifukwa chakuti amanena: “Sudzatikhudza Moto koma masiku ochepa basi.” Ndipo zawanyenga pa chipembedzo chawo zomwe adali kupeka (kuti adzakhululukidwa kapena kulangidwa masiku ochepa okha). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 3

فَكَيۡفَ إِذَا جَمَعۡنَٰهُمۡ لِيَوۡمٖ لَّا رَيۡبَ فِيهِ وَوُفِّيَتۡ كُلُّ نَفۡسٖ مَّا كَسَبَتۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ

Kodi zidzakhala zotani pamene tidzawasonkhanitsa tsiku lopanda chikaiko? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira pa zomwe udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 3

قُلِ ٱللَّهُمَّ مَٰلِكَ ٱلۡمُلۡكِ تُؤۡتِي ٱلۡمُلۡكَ مَن تَشَآءُ وَتَنزِعُ ٱلۡمُلۡكَ مِمَّن تَشَآءُ وَتُعِزُّ مَن تَشَآءُ وَتُذِلُّ مَن تَشَآءُۖ بِيَدِكَ ٱلۡخَيۡرُۖ إِنَّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Nena “E Mbuye wanga! Mwini ufumu wonse. Mumapereka ufumu kwa yemwe mwamfuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa yemwe mwamfuna. Mumapereka ulemelero kwa yemwe mwamfuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamfuna. Ubwino wonse uli m’manja Mwanu. Ndithudi, Inu ndinu Wokhonza chilichonse.” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 3

تُولِجُ ٱلَّيۡلَ فِي ٱلنَّهَارِ وَتُولِجُ ٱلنَّهَارَ فِي ٱلَّيۡلِۖ وَتُخۡرِجُ ٱلۡحَيَّ مِنَ ٱلۡمَيِّتِ وَتُخۡرِجُ ٱلۡمَيِّتَ مِنَ ٱلۡحَيِّۖ وَتَرۡزُقُ مَن تَشَآءُ بِغَيۡرِ حِسَابٖ

(Inu) mumalowetsa usiku mu usana (ndikukhala usana wautali monga m’nyengo yotentha). Ndipo mumalowetsa usana mu usiku (nkukhala usiku wautali monga m’nyengo yachisanu). Mumatulutsa cha moyo m’chakufa; ndipo mumatulutsa chakufa m’chamoyo. Ndipo mumapatsa rizq (chakudya) amene mwamfuna mopanda chiwerengero.” info
التفاسير:

external-link copy
28 : 3

لَّا يَتَّخِذِ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلۡكَٰفِرِينَ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَۖ وَمَن يَفۡعَلۡ ذَٰلِكَ فَلَيۡسَ مِنَ ٱللَّهِ فِي شَيۡءٍ إِلَّآ أَن تَتَّقُواْ مِنۡهُمۡ تُقَىٰةٗۗ وَيُحَذِّرُكُمُ ٱللَّهُ نَفۡسَهُۥۗ وَإِلَى ٱللَّهِ ٱلۡمَصِيرُ

Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi). info
التفاسير:

external-link copy
29 : 3

قُلۡ إِن تُخۡفُواْ مَا فِي صُدُورِكُمۡ أَوۡ تُبۡدُوهُ يَعۡلَمۡهُ ٱللَّهُۗ وَيَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَا فِي ٱلۡأَرۡضِۗ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ

Nena: “Ngati mubisa zomwe zili m’zifuwa zanu, kapena kuzionetsa (poyera), Allah akuzidziwa. Iye akudziwa zonse zakumwamba ndi zapansi. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.” info
التفاسير: