ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا

رقم الصفحة:close

external-link copy
90 : 23

بَلۡ أَتَيۡنَٰهُم بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ

Koma tawabweretsera choonadi; ndithu iwo ngabodza (potsutsana ndi choonadicho). info
التفاسير:

external-link copy
91 : 23

مَا ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ مِن وَلَدٖ وَمَا كَانَ مَعَهُۥ مِنۡ إِلَٰهٍۚ إِذٗا لَّذَهَبَ كُلُّ إِلَٰهِۭ بِمَا خَلَقَ وَلَعَلَا بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ

Allah sadadzipangire mwana, ndipo padalibe pamodzi ndi Iye mulungu (wina), ngati zikadakhala choncho ndiye kuti mulungu aliyense akadatenga zimene adalenga, ndipo milungu ina ikadaipambana milungu inzawo (polimbanirana ufumu), Allah wapatukana nazo kwambiri zimene akusimbazo. info
التفاسير:

external-link copy
92 : 23

عَٰلِمِ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ فَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ

Wodziwa zamseri ndi zapoyera; watukuka ku zimene akumphatikiza nazozo. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 23

قُل رَّبِّ إِمَّا تُرِيَنِّي مَا يُوعَدُونَ

Nena: “E Mbuye wanga! Ngati mungandionetse zomwe akulonjezedwa (ndikadali ndi moyo), info
التفاسير:

external-link copy
94 : 23

رَبِّ فَلَا تَجۡعَلۡنِي فِي ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ

E Mbuye wanga! Musandiyike m’gulu la anthu osalungama.” info
التفاسير:

external-link copy
95 : 23

وَإِنَّا عَلَىٰٓ أَن نُّرِيَكَ مَا نَعِدُهُمۡ لَقَٰدِرُونَ

Ndipo ndithu Ife ndi Wokhoza kukuonetsa (chilango) chimene tikuwalonjeza. info
التفاسير:

external-link copy
96 : 23

ٱدۡفَعۡ بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ ٱلسَّيِّئَةَۚ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَصِفُونَ

Chotsa zoipa (zimene akukuchitira) powabwezera zabwino; Ife tikudziwa zimene akunena. info
التفاسير:

external-link copy
97 : 23

وَقُل رَّبِّ أَعُوذُ بِكَ مِنۡ هَمَزَٰتِ ٱلشَّيَٰطِينِ

Ndipo nena: “E Mbuye wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi Inu kumanong’onong’o a satana.” info
التفاسير:

external-link copy
98 : 23

وَأَعُوذُ بِكَ رَبِّ أَن يَحۡضُرُونِ

“Ndiponso ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye wanga kuti asandidzere.” info
التفاسير:

external-link copy
99 : 23

حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَهُمُ ٱلۡمَوۡتُ قَالَ رَبِّ ٱرۡجِعُونِ

Kufikira m’modzi wawo ikam’dzera imfa, amanena: “Mbuye wanga! Ndibwezereni (ku moyo wa pa dziko),” info
التفاسير:

external-link copy
100 : 23

لَعَلِّيٓ أَعۡمَلُ صَٰلِحٗا فِيمَا تَرَكۡتُۚ كَلَّآۚ إِنَّهَا كَلِمَةٌ هُوَ قَآئِلُهَاۖ وَمِن وَرَآئِهِم بَرۡزَخٌ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ

“Kuti ndikachite zabwino pa zimene ndidasiya.” (Angelo amayankha kuti): “Iyayi! Ndithu awa ndi mawu basi amene iye akuyankhula (imfa ikamfika).” Ndipo patsogolo pawo pali chiyembekezo; (moyo wamasautso kwa oipa; ndipo wamtendere kwa abwino) kufikira tsiku limene adzaukitsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
101 : 23

فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَلَآ أَنسَابَ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ وَلَا يَتَسَآءَلُونَ

Choncho, lipenga likadzaimbidwa, sipadzakhala chibale pakati pawo tsiku limenelo, ndipo sadzafunsana. info
التفاسير:

external-link copy
102 : 23

فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ

Tsono omwe mlingo (wa zochita zawo zabwino) udzalemere, iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير:

external-link copy
103 : 23

وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فِي جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ

Ndipo omwe miyeso yawo (ya zochita zabwino) idzatsike, iwowo ndi omwe adadziluzitsa okha; adzakhala ku Jahannam nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
104 : 23

تَلۡفَحُ وُجُوهَهُمُ ٱلنَّارُ وَهُمۡ فِيهَا كَٰلِحُونَ

Moto ukawawula nkhope zawo, ndipo adzakhala m’menemo uku mano ali pamtunda. info
التفاسير: