《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

页码:close

external-link copy
14 : 9

قَٰتِلُوهُمۡ يُعَذِّبۡهُمُ ٱللَّهُ بِأَيۡدِيكُمۡ وَيُخۡزِهِمۡ وَيَنصُرۡكُمۡ عَلَيۡهِمۡ وَيَشۡفِ صُدُورَ قَوۡمٖ مُّؤۡمِنِينَ

Menyanani nao; Allah awalanga kupyolera m’manja anu, ndipo awasambula ndi kukupulumutsani kwa iwo ndi kuchiritsa kuwawidwa (komwe kudali) m’mitima mwa anthu okhulupirira (chifukwa cha masautso omwe adawapeza kwa iwo). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 9

وَيُذۡهِبۡ غَيۡظَ قُلُوبِهِمۡۗ وَيَتُوبُ ٱللَّهُ عَلَىٰ مَن يَشَآءُۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ

Ndi kuchotsa mkwiyo wa m’mitima mwawo (Asilamu). Ndi kuti Allah Alandire kulapa kwa amene wamfuna. Ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya. info
التفاسير:

external-link copy
16 : 9

أَمۡ حَسِبۡتُمۡ أَن تُتۡرَكُواْ وَلَمَّا يَعۡلَمِ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ جَٰهَدُواْ مِنكُمۡ وَلَمۡ يَتَّخِذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَلَا رَسُولِهِۦ وَلَا ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَلِيجَةٗۚ وَٱللَّهُ خَبِيرُۢ بِمَا تَعۡمَلُونَ

Kodi mukuganiza kuti mungosiidwa chabe Allah asanawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo mwa inu ndi amene sachita ubwenzi (ndi wina wake) kupatula Allah ndi Mtumiki wake ndi okhulupirira? Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 9

مَا كَانَ لِلۡمُشۡرِكِينَ أَن يَعۡمُرُواْ مَسَٰجِدَ ٱللَّهِ شَٰهِدِينَ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِم بِٱلۡكُفۡرِۚ أُوْلَٰٓئِكَ حَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡ وَفِي ٱلنَّارِ هُمۡ خَٰلِدُونَ

Nkosayenera kwa Amushirikina kukhala (ndi udindo) woyang’anira Misikiti ya Allah pomwe iwo akudzichitira okha umboni kuti ngosakhulupirira. Awo (ndi omwe) zochita zawo zabwino zapita pachabe. Ndipo iwo ku Moto adzakhala nthawi yaitali. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 9

إِنَّمَا يَعۡمُرُ مَسَٰجِدَ ٱللَّهِ مَنۡ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَأَقَامَ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتَى ٱلزَّكَوٰةَ وَلَمۡ يَخۡشَ إِلَّا ٱللَّهَۖ فَعَسَىٰٓ أُوْلَٰٓئِكَ أَن يَكُونُواْ مِنَ ٱلۡمُهۡتَدِينَ

Ndithu oyang’anira Misikiti ya Allah ndi kuiyendera ndi amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumapemphera Swala ndi kupereka chopereka (Zakaat) ndipo saopa aliyense koma Allah yekha. Choncho, iwowo ndi amene akuyembekezeka kukhala mwa oongoka. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 9

۞ أَجَعَلۡتُمۡ سِقَايَةَ ٱلۡحَآجِّ وَعِمَارَةَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ كَمَنۡ ءَامَنَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِ وَجَٰهَدَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۚ لَا يَسۡتَوُۥنَ عِندَ ٱللَّهِۗ وَٱللَّهُ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ

Kodi kumwetsa madzi (anthu) ochita Hajj ndi kusunga Msikiti Wopatulika mukukuyesa kuti nkofanana ndi yemwe wakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumenya nkhondo pa njira Ya Allah? Sangakhale ofanana kwa Allah. Ndipo Allah saongola anthu ochita zolakwa. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 9

ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَهَاجَرُواْ وَجَٰهَدُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ بِأَمۡوَٰلِهِمۡ وَأَنفُسِهِمۡ أَعۡظَمُ دَرَجَةً عِندَ ٱللَّهِۚ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَآئِزُونَ

Amene akhulupirira, ndi kusamuka, ndi kumenya nkhondo pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi matupi awo, ali ndi ulemelero waukulu kwa Allah. Iwowo ndiwo opambana. info
التفاسير: