《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

页码:close

external-link copy
196 : 7

إِنَّ وَلِـِّۧيَ ٱللَّهُ ٱلَّذِي نَزَّلَ ٱلۡكِتَٰبَۖ وَهُوَ يَتَوَلَّى ٱلصَّٰلِحِينَ

“Ndithu Mtetezi wanga ndi Allah, Yemwe wavumbulutsa buku (ili lopatulika). Ndipo Iye amawateteza ochita zabwino.” info
التفاسير:

external-link copy
197 : 7

وَٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَكُمۡ وَلَآ أَنفُسَهُمۡ يَنصُرُونَ

“Ndipo omwe mukuwapembedza kusiya Iye (Allah,) sangathe kukupulumutsani ndiponso sangathe kudzipulumutsa okha.” info
التفاسير:

external-link copy
198 : 7

وَإِن تَدۡعُوهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ لَا يَسۡمَعُواْۖ وَتَرَىٰهُمۡ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ وَهُمۡ لَا يُبۡصِرُونَ

Ngati mutawaitanira ku chiwongoko, sangamve; koma uwaona akukuyang’ana koma pomwe iwo sakuona. info
التفاسير:

external-link copy
199 : 7

خُذِ ٱلۡعَفۡوَ وَأۡمُرۡ بِٱلۡعُرۡفِ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡجَٰهِلِينَ

Khala ndi khalidwe lokhululuka, lamula zabwino ndipo dzipatule ku mbuli. info
التفاسير:

external-link copy
200 : 7

وَإِمَّا يَنزَغَنَّكَ مِنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ نَزۡغٞ فَٱسۡتَعِذۡ بِٱللَّهِۚ إِنَّهُۥ سَمِيعٌ عَلِيمٌ

Ndipo ngati manong’onong’o a satana atakuvutitsa, dzitchinjirize ndi Allah. Ndithu Iye Ngwakumva, Ngodziwa. info
التفاسير:

external-link copy
201 : 7

إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱتَّقَوۡاْ إِذَا مَسَّهُمۡ طَٰٓئِفٞ مِّنَ ٱلشَّيۡطَٰنِ تَذَكَّرُواْ فَإِذَا هُم مُّبۡصِرُونَ

Ndithu amene akuopa (Allah), udyerekezi wa satana ukawakhudza amakumbukira (Allah), nkuona (njira yotulukira muudyerekezi wakewo). info
التفاسير:

external-link copy
202 : 7

وَإِخۡوَٰنُهُمۡ يَمُدُّونَهُمۡ فِي ٱلۡغَيِّ ثُمَّ لَا يُقۡصِرُونَ

Koma anzawo (omwe ali oipa) amawalimbikitsa m’machimo, ndipo kenako saleka (kupitiriza machimowo). info
التفاسير:

external-link copy
203 : 7

وَإِذَا لَمۡ تَأۡتِهِم بِـَٔايَةٖ قَالُواْ لَوۡلَا ٱجۡتَبَيۡتَهَاۚ قُلۡ إِنَّمَآ أَتَّبِعُ مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ مِن رَّبِّيۚ هَٰذَا بَصَآئِرُ مِن رَّبِّكُمۡ وَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ

Ngati siudawabweretsere chozizwitsa, akunena: “Bwanji wosachibweretsa pa iwe wekha? Nena: “Ndithudi ndikutsatira zimene zikuvumbulitsidwa kwa ine kuchokera kwa Mbuye wanga. (Sindichita chinthu mwa ine ndekha). Iyi (Qur’an) ndi umboni (waukulu pa zoyankhula zanga) kuchokera kwa Mbuye wanu. (Izo) ndi chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
204 : 7

وَإِذَا قُرِئَ ٱلۡقُرۡءَانُ فَٱسۡتَمِعُواْ لَهُۥ وَأَنصِتُواْ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ

Ndipo Qur’an ikamawerengedwa, mvetserani (mwatcheru) ndi kukhala chete, kuti muchitiridwe chifundo. info
التفاسير:

external-link copy
205 : 7

وَٱذۡكُر رَّبَّكَ فِي نَفۡسِكَ تَضَرُّعٗا وَخِيفَةٗ وَدُونَ ٱلۡجَهۡرِ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ بِٱلۡغُدُوِّ وَٱلۡأٓصَالِ وَلَا تَكُن مِّنَ ٱلۡغَٰفِلِينَ

Ndipo mtchule Mbuye wako mu mtima mwako modzichepetsa, mwa mantha ndi mosakweza mawu m’mawa ndi madzulo; ndipo usakhale mwa osalabadila (malamulo a Allah). info
التفاسير:

external-link copy
206 : 7

إِنَّ ٱلَّذِينَ عِندَ رَبِّكَ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَيُسَبِّحُونَهُۥ وَلَهُۥ يَسۡجُدُونَۤ۩

Ndithu amene ali kwa Mbuye wako, (angelo), sadzitukumula posiya kumpembedza (Mbuye wawo, koma iwo) amam’lemekeza ndi kumlambira. info
التفاسير: