《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

external-link copy
138 : 6

وَقَالُواْ هَٰذِهِۦٓ أَنۡعَٰمٞ وَحَرۡثٌ حِجۡرٞ لَّا يَطۡعَمُهَآ إِلَّا مَن نَّشَآءُ بِزَعۡمِهِمۡ وَأَنۡعَٰمٌ حُرِّمَتۡ ظُهُورُهَا وَأَنۡعَٰمٞ لَّا يَذۡكُرُونَ ٱسۡمَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَا ٱفۡتِرَآءً عَلَيۡهِۚ سَيَجۡزِيهِم بِمَا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ

Iwo akuti: “Ziweto izi ndi mbewu izi, nzoletsedwa; palibe angazidye koma amene tawafuna (kuti adye),” zonsezi mkuyankhula kwawo kwachabe. Ndipo (amanenanso): “Ziweto izi, misana yake njoletsedwa (kukwerapo).” Ndipo pa ziweto zina satchula dzina la Allah pozizinga; kungompekera bodza Iye. Ndipo posachedwa adzawalipira pa zomwe adali kupeka. info
التفاسير: