《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

页码:close

external-link copy
15 : 34

لَقَدۡ كَانَ لِسَبَإٖ فِي مَسۡكَنِهِمۡ ءَايَةٞۖ جَنَّتَانِ عَن يَمِينٖ وَشِمَالٖۖ كُلُواْ مِن رِّزۡقِ رَبِّكُمۡ وَٱشۡكُرُواْ لَهُۥۚ بَلۡدَةٞ طَيِّبَةٞ وَرَبٌّ غَفُورٞ

Ndithu padali phunziro pa anthu a dziko la Saba mokhala mwawo: (Padali) minda iwiri, kumanja ndi kumanzere. (Tidati:) “Idyani zakudya zaulere zochokera kwa Mbuye wanu, ndipo mthokozeni. Mudzi wabwino ndi Mbuye Wokhululuka.” info
التفاسير:

external-link copy
16 : 34

فَأَعۡرَضُواْ فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ سَيۡلَ ٱلۡعَرِمِ وَبَدَّلۡنَٰهُم بِجَنَّتَيۡهِمۡ جَنَّتَيۡنِ ذَوَاتَيۡ أُكُلٍ خَمۡطٖ وَأَثۡلٖ وَشَيۡءٖ مِّن سِدۡرٖ قَلِيلٖ

Koma adanyozera (lamulo la Allah); choncho tidawatumizira chigumula champhamvu chamadzi otchingidwa (chomwe chidawamiza ndi kuononga minda yawo). Ndipo tidawasinthira minda yawo (yabwino) kukhala minda iwiri yazipatso zowawa, ndi mitengo ya bwemba ndi mitengo pang’ono ya masawu.[335] info

[335] Anthu am’mudzi wa Saba’a komwe nkudziko la Yemeni, Allah adawapatsa madalitso ambiri pamene iwo amatsatira malamuio Ake ndi kumthokoza. Adawadalitsa ndi minda ya zipatso zokoma zomwe zidalibe nyengo yeniyeni yobalira, kotero kuti azimayi ankangosenza madengu nkumangoyenda pansi pa mitengo ndipo mwadzidzidzi ankangoona madengu ali odzaza ndi zipatso zoyoyoka m’mitengoyo. Koma pamene adasiya kumuyamika Allah ndi kutsatira malamulo Ake, adawaonongera mindayo ndi chigumula ndi kuwasinthitsira zipatso zawo ndi zipatso zopanda pake.

التفاسير:

external-link copy
17 : 34

ذَٰلِكَ جَزَيۡنَٰهُم بِمَا كَفَرُواْۖ وَهَلۡ نُجَٰزِيٓ إِلَّا ٱلۡكَفُورَ

Amenewo ndiwo malipiro tidawalipira chifukwa cha kusathokoza kwawo (mtendere wa Allah). Ndipo Ife sitilipira zoterezi koma kwa okhawo osathokoza. info
التفاسير:

external-link copy
18 : 34

وَجَعَلۡنَا بَيۡنَهُمۡ وَبَيۡنَ ٱلۡقُرَى ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَا قُرٗى ظَٰهِرَةٗ وَقَدَّرۡنَا فِيهَا ٱلسَّيۡرَۖ سِيرُواْ فِيهَا لَيَالِيَ وَأَيَّامًا ءَامِنِينَ

Ndipo pakati pawo ndi pakati pa midzi imene tidaidalitsa, tidaikapo midzi imene idali yoonekera; ndipo tidapima m’menemo malo apaulendo. (kotero kuti amachoka malo nkufika malo ena mosavutika. Tidawauza): “Yendani m’menemo usiku ndi usana mwamtendere.” info
التفاسير:

external-link copy
19 : 34

فَقَالُواْ رَبَّنَا بَٰعِدۡ بَيۡنَ أَسۡفَارِنَا وَظَلَمُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَحَادِيثَ وَمَزَّقۡنَٰهُمۡ كُلَّ مُمَزَّقٍۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّكُلِّ صَبَّارٖ شَكُورٖ

Koma (adauda mtendere umenewu;) adati: “E Mbuye wathu! Talikitsani ntunda pakati pa maulendo athu; (kuyandikirana kwa midzi, sikukutisonyeza kuti tili pa ulendo).” Ndipo adadzichitira okha zoipa. Choncho tidawachita kukhala miyambi (imene anthu a pambuyo ankauzana pakati pawo), ndipo tidawabalalitsa; kubalalikana zedi. (Ena adathawira dziko ili, ena dziko lina). Ndithu m’zimenezo muli malingaliro kwa yense wopirira kwabasi ndi wothokoza kwambiri. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 34

وَلَقَدۡ صَدَّقَ عَلَيۡهِمۡ إِبۡلِيسُ ظَنَّهُۥ فَٱتَّبَعُوهُ إِلَّا فَرِيقٗا مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ

Ndipo ndithu Iblis adatsimikiza ganizo lake pa iwo choncho adamtsatira kupatula gulu la okhulupirira (moona). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 34

وَمَا كَانَ لَهُۥ عَلَيۡهِم مِّن سُلۡطَٰنٍ إِلَّا لِنَعۡلَمَ مَن يُؤۡمِنُ بِٱلۡأٓخِرَةِ مِمَّنۡ هُوَ مِنۡهَا فِي شَكّٖۗ وَرَبُّكَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٍ حَفِيظٞ

Ndipo iye adalibe nyonga pa iwo, koma chifukwa chakuti tionetse poyera ndani wokhulupirira tsiku la chimaliziro ndiponso ndani amene akulikaikira. Ndipo Mbuye wako Ngosunga chilichonse.[336] info

[336] Pamene satana adatha kumsokeretsa Adam adaganizanso kuti adzatha kuwasokeretsa ana ake. Ndipo ana a Adam adamtsatiradi satanayo monga momwe iye ankaganizira. Komatu satana alibe mphamvu zomkakamizira mwana wa Adam kuti amtsate koma amangomuitana kupyolera m’kukometsera zilakolako zoipa.

التفاسير:

external-link copy
22 : 34

قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ لَا يَمۡلِكُونَ مِثۡقَالَ ذَرَّةٖ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَلَا فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا لَهُمۡ فِيهِمَا مِن شِرۡكٖ وَمَا لَهُۥ مِنۡهُم مِّن ظَهِيرٖ

Nena: “Itanani amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Allah (kuti akuthandizeni. Koma sangakuthandizeni chilichonse; pakuti iwo) alibe ngakhale kachinthu ka kumwamba ndi pansi kolemera ngati nyelere yaing’ono kwambiri; m’menemo iwo alibe gawo lililonse (lothandizana ndi Allah), ndipo ngakhale Iyenso alibe mthandizi wochokera mwa iwo. info
التفاسير: