《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

external-link copy
26 : 33

وَأَنزَلَ ٱلَّذِينَ ظَٰهَرُوهُم مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ مِن صَيَاصِيهِمۡ وَقَذَفَ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلرُّعۡبَ فَرِيقٗا تَقۡتُلُونَ وَتَأۡسِرُونَ فَرِيقٗا

Ndipo adawatsitsa m’malinga mwawo amene adathandiza adaniwo mwa anthu a buku (Ayuda). Ndipo adathira mantha m’mitima mwawo. Ena mumawapha; ndipo ena mumawagwira.[321] info

[321] Awa ndi Ayuda amene adasakanikirana ndi osakhulupilira (akafiri) a Chiarabu ochokera mu mtundu wa Banu Quraidhwa omwe adali ndi mapangano ndi Mtumiki (s.a.w) okhalirana mwa mtendere. Koma pamene adaswa mapangano pothandizana ndi adani a Mtumiki kuthira nkhondo Asilamu Mtumiki Muhammad (s.a.w) adawapitira ku malinga awo. Ndipo ena adawapha, pomwe ena adawagwira monga akaidi a pankhondo.

التفاسير: