《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

页码:close

external-link copy
18 : 23

وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٖ فَأَسۡكَنَّٰهُ فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَإِنَّا عَلَىٰ ذَهَابِۭ بِهِۦ لَقَٰدِرُونَ

Ndipo tatsitsa madzi mwamuyeso kuchokera kumwamba, ndi kuwakhazikitsa m’nthaka; ndipo ndithu Ife ndi okhoza kuwachotsa (kuti musathandizike nawo, koma sitidachite zimenezo chifukwa chokuchitirani chifundo). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 23

فَأَنشَأۡنَا لَكُم بِهِۦ جَنَّٰتٖ مِّن نَّخِيلٖ وَأَعۡنَٰبٖ لَّكُمۡ فِيهَا فَوَٰكِهُ كَثِيرَةٞ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ

Ndi madzi amenewo, tidakupangirani minda ya kanjedza ndi mpesa, m’menemo inu mulinazo zipatso zambiri; ndipo mwazimenezo mumadya. info
التفاسير:

external-link copy
20 : 23

وَشَجَرَةٗ تَخۡرُجُ مِن طُورِ سَيۡنَآءَ تَنۢبُتُ بِٱلدُّهۡنِ وَصِبۡغٖ لِّلۡأٓكِلِينَ

Ndipo (tidakupangirani) mtengo womera pa phiri la Sinai, womwe umatulutsa mafuta; ndipo ndindiwo kwa amene amadya. (Mtengo wake ndi mzitona). info
التفاسير:

external-link copy
21 : 23

وَإِنَّ لَكُمۡ فِي ٱلۡأَنۡعَٰمِ لَعِبۡرَةٗۖ نُّسۡقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهَا وَلَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ كَثِيرَةٞ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ

Ndipo ndithu m’ziweto muli lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwake; ndipo m’zimenezo mukupeza zothandiza zambiri; ndipo zina mwa izo mumadya. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 23

وَعَلَيۡهَا وَعَلَى ٱلۡفُلۡكِ تُحۡمَلُونَ

Ndipo pa msana pa izo ndi pamwamba pa zombo, mumanyamulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
23 : 23

وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ

Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah! Mulibe mulungu wina woti nkumpembedza kupatula Iye. Kodi simuopa (chilango Chake?) info
التفاسير:

external-link copy
24 : 23

فَقَالَ ٱلۡمَلَؤُاْ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ مَا هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُرِيدُ أَن يَتَفَضَّلَ عَلَيۡكُمۡ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَأَنزَلَ مَلَٰٓئِكَةٗ مَّا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِيٓ ءَابَآئِنَا ٱلۡأَوَّلِينَ

Akuluakulu mwa anthu ake amene sadakhulupirire, adati: “Uyu sali kanthu, koma ndi munthu ngati inu; akufuna kuti adzipezere ubwino pa inu; ndipo Allah akadafuna (kukuphunzitsani) akadatuma angelo. Zoterezi sitidamvepo kumakolo athu akale.” info
التفاسير:

external-link copy
25 : 23

إِنۡ هُوَ إِلَّا رَجُلُۢ بِهِۦ جِنَّةٞ فَتَرَبَّصُواْ بِهِۦ حَتَّىٰ حِينٖ

“Uyu sali kanthu, koma ndi munthu wamisala; choncho muyembekezereni mpaka nthawi (yofera.”) info
التفاسير:

external-link copy
26 : 23

قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي بِمَا كَذَّبُونِ

(Nuh) adati: “Mbuye wanga ndipulumutseni pazomwe anditsutsa!” info
التفاسير:

external-link copy
27 : 23

فَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِ أَنِ ٱصۡنَعِ ٱلۡفُلۡكَ بِأَعۡيُنِنَا وَوَحۡيِنَا فَإِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ فَٱسۡلُكۡ فِيهَا مِن كُلّٖ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ مِنۡهُمۡۖ وَلَا تُخَٰطِبۡنِي فِي ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ إِنَّهُم مُّغۡرَقُونَ

Choncho tidamuvumbulutsira (mawu akuti): “Panga chombo moyang’aniridwa ndi kudziwitsidwa ndi Ife.” Ndipo lamulo Lathu likadza ndi kufwamphuka madzi mu uvuni, lowetsa mkati mwake (mwa chombocho) chilichonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi ndi banja lako, kupatula yemwe liwu latsogola pa iye kuti aonongeke mwa iwo. Ndipo usandilankhule za omwe adzichitira (okha) zoipa ndithu iwo amizidwa (m’madzi). info
التفاسير: