《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。

external-link copy
108 : 12

قُلۡ هَٰذِهِۦ سَبِيلِيٓ أَدۡعُوٓاْ إِلَى ٱللَّهِۚ عَلَىٰ بَصِيرَةٍ أَنَا۠ وَمَنِ ٱتَّبَعَنِيۖ وَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُشۡرِكِينَ

Nena: “Iyi ndi njira yanga. Ndikuitanira kwa Allah mwa nzeru zokwanira, ine ndi omwe akunditsata. Ndithu Allah wapatukana (ndi mbiri zopunguka). Ndipo ine sindili mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).”[235] info

[235] Apa Mtumiki (s.a.w) akuuzidwa kuti awauze anthu kuti iye pamodzi ndi amene akumutsata kuti amalalikira Chisilamu kwa anthu popereka kwa anthuwo mitsutso yanzeru, ndikuperekanso zisonyezo ndi maumboni amphamvu. Sibwino Msilamu kutsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino. Qur’an ikunenetsa kuti osatsatira chinthu popanda kuchidziwa bwinobwino pokhapokha chinthucho chitanenedwa ndi Allah kapena Mtumiki Wake.

التفاسير: