Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Al-Qiyâmah

external-link copy
1 : 75

لَآ أُقۡسِمُ بِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ

Ndikulumbilira tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 75

وَلَآ أُقۡسِمُ بِٱلنَّفۡسِ ٱللَّوَّامَةِ

Ndikulumbiliranso mzimu wodzidzudzula (pa cholakwa chimene wachita. Ndithu mudzaukitsidwa; mafupa anu omwazikana atasonkhanitsidwa.) info
التفاسير:

external-link copy
3 : 75

أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَلَّن نَّجۡمَعَ عِظَامَهُۥ

Kodi munthu akuganiza kuti Ife (Amene tidamlenga kuchokera popanda chilichonse) sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake (ofumbwa)? info
التفاسير:

external-link copy
4 : 75

بَلَىٰ قَٰدِرِينَ عَلَىٰٓ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُۥ

Iyayi, Ife tikhoza (kutisonkhanitsa) ndi kutilongosola bwino timizere takunsonga kwa zala zake. (Mafupa ake ndiye osanena)! info
التفاسير:

external-link copy
5 : 75

بَلۡ يُرِيدُ ٱلۡإِنسَٰنُ لِيَفۡجُرَ أَمَامَهُۥ

Koma munthu akufuna kuti apitirize kuchimwa (mmasiku akudza) mtsogolo mwake. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 75

يَسۡـَٔلُ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلۡقِيَٰمَةِ

Akufunsa (mwa chipongwe): “Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?” info
التفاسير:

external-link copy
7 : 75

فَإِذَا بَرِقَ ٱلۡبَصَرُ

Pamene maso adzangoti tong’oo (ndi mantha), info
التفاسير:

external-link copy
8 : 75

وَخَسَفَ ٱلۡقَمَرُ

Ndi kuchoka kuwala kwa mwezi, info
التفاسير:

external-link copy
9 : 75

وَجُمِعَ ٱلشَّمۡسُ وَٱلۡقَمَرُ

Ndipo dzuwa ndi mwezi ndikusonkhanitsidwa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 75

يَقُولُ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذٍ أَيۡنَ ٱلۡمَفَرُّ

Munthu adzanena tsiku limenelo: “Nkuti kothawira (chilangochi?)” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 75

كَلَّا لَا وَزَرَ

(Adzauzidwa): “Iyayi, (iwe munthu) palibe pothawira (pako)!” info
التفاسير:

external-link copy
12 : 75

إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمُسۡتَقَرُّ

Tsiku limenelo kobwerera (anthu) ndi kwa Mbuye wako basi. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 75

يُنَبَّؤُاْ ٱلۡإِنسَٰنُ يَوۡمَئِذِۭ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ

Tsiku limenelo munthu adzauzidwa zochita zake zimene adazitsogoza ndi zimene adazichedwetsa. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 75

بَلِ ٱلۡإِنسَٰنُ عَلَىٰ نَفۡسِهِۦ بَصِيرَةٞ

Koma munthu adzadzichitira umboni yekha pa mzimu wake. info
التفاسير:

external-link copy
15 : 75

وَلَوۡ أَلۡقَىٰ مَعَاذِيرَهُۥ

Ngakhale atapereka madandaulo ake (otani kuti apulumuke nawo sadzapulumuka). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 75

لَا تُحَرِّكۡ بِهِۦ لِسَانَكَ لِتَعۡجَلَ بِهِۦٓ

Usaigwedezere (Qur’an) lirime lako (pamene ikuvumbulutsidwa) kuti uifulumilire (kuiwerenga ndi kuisunga mu mtima). info
التفاسير:

external-link copy
17 : 75

إِنَّ عَلَيۡنَا جَمۡعَهُۥ وَقُرۡءَانَهُۥ

Ndithu ndiudindo wathu kuisonkhanitsa (mu mtima mwako) ndi kukhazikitsa kawerengedwe kake (palirime lako). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 75

فَإِذَا قَرَأۡنَٰهُ فَٱتَّبِعۡ قُرۡءَانَهُۥ

Choncho pamene tikukuwerengera iwe tsatira kuwerenga kwakeko (uku uli chete). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 75

ثُمَّ إِنَّ عَلَيۡنَا بَيَانَهُۥ

Kenako, ndithu ndiudindo Wathu kulongosola (zimene siukumvetsa), info
التفاسير:

external-link copy
20 : 75

كَلَّا بَلۡ تُحِبُّونَ ٱلۡعَاجِلَةَ

Iyayi koma mukukonda moyo wa pa dziko. info
التفاسير:

external-link copy
21 : 75

وَتَذَرُونَ ٱلۡأٓخِرَةَ

Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
22 : 75

وُجُوهٞ يَوۡمَئِذٖ نَّاضِرَةٌ

Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zowala, info
التفاسير:

external-link copy
23 : 75

إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةٞ

Zili kumuyang’ana Mbuye wawo. info
التفاسير:

external-link copy
24 : 75

وَوُجُوهٞ يَوۡمَئِذِۭ بَاسِرَةٞ

Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 75

تَظُنُّ أَن يُفۡعَلَ بِهَا فَاقِرَةٞ

Zikuyembekezeka kuti zilandira tsoka lodula msana. info
التفاسير:

external-link copy
26 : 75

كَلَّآ إِذَا بَلَغَتِ ٱلتَّرَاقِيَ

Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa). info
التفاسير:

external-link copy
27 : 75

وَقِيلَ مَنۡۜ رَاقٖ

Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse! info
التفاسير:

external-link copy
28 : 75

وَظَنَّ أَنَّهُ ٱلۡفِرَاقُ

Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi), info
التفاسير:

external-link copy
29 : 75

وَٱلۡتَفَّتِ ٱلسَّاقُ بِٱلسَّاقِ

Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu). info
التفاسير:

external-link copy
30 : 75

إِلَىٰ رَبِّكَ يَوۡمَئِذٍ ٱلۡمَسَاقُ

Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako. info
التفاسير:

external-link copy
31 : 75

فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ

Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu), info
التفاسير:

external-link copy
32 : 75

وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ

Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza. info
التفاسير:

external-link copy
33 : 75

ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ يَتَمَطَّىٰٓ

Kenaka adapita kubanja lake (uku akuyenda) monyada. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 75

أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰ

Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi! info
التفاسير:

external-link copy
35 : 75

ثُمَّ أَوۡلَىٰ لَكَ فَأَوۡلَىٰٓ

Ndiponso kuonongeka nkwako! kuonongeka zedi! info
التفاسير:

external-link copy
36 : 75

أَيَحۡسَبُ ٱلۡإِنسَٰنُ أَن يُتۡرَكَ سُدًى

Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)? info
التفاسير:

external-link copy
37 : 75

أَلَمۡ يَكُ نُطۡفَةٗ مِّن مَّنِيّٖ يُمۡنَىٰ

Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)? info
التفاسير:

external-link copy
38 : 75

ثُمَّ كَانَ عَلَقَةٗ فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ

Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu). info
التفاسير:

external-link copy
39 : 75

فَجَعَلَ مِنۡهُ ٱلزَّوۡجَيۡنِ ٱلذَّكَرَ وَٱلۡأُنثَىٰٓ

Ndipo adalenga kuchokera mmenemo mitundu iwiri: mwamuna ndi mkazi. info
التفاسير:

external-link copy
40 : 75

أَلَيۡسَ ذَٰلِكَ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰ

Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa? info
التفاسير: