[358] (Ndime 2-3) Khalidwe la munthu limene limakwiyitsa Allah kwambiri ndiko kunena zokoma chikhalirecho zochita zili zoipa. Amawanyenga anthu ndi mawu otsekemera koma zochita zake ndizachinyengo zokhazokha. Munthu wa makhalidwe otere, malipiro ake ndi kulowa ku nthukutira ya Moto. Choncho zochita zanu zifanane ndi zimene mukuyankhula. Apeweni makhalidwe achiphamaso.
[359] Allah akufuna kuti Asilamu akhale dzanja limodzi pofalitsa Chisilamu, agwire ntchito yokomera gulu lonse mothangatana.
[360] (Ndime 8-9) Allah akulonjeza kuti Chisilamu chidzapambana zipembedzo zonse ngakhale osakhulupilira akuchithira nkhondo.