Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

external-link copy
151 : 6

۞ قُلۡ تَعَالَوۡاْ أَتۡلُ مَا حَرَّمَ رَبُّكُمۡ عَلَيۡكُمۡۖ أَلَّا تُشۡرِكُواْ بِهِۦ شَيۡـٔٗاۖ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنٗاۖ وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُم مِّنۡ إِمۡلَٰقٖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُكُمۡ وَإِيَّاهُمۡۖ وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلۡفَوَٰحِشَ مَا ظَهَرَ مِنۡهَا وَمَا بَطَنَۖ وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۚ ذَٰلِكُمۡ وَصَّىٰكُم بِهِۦ لَعَلَّكُمۡ تَعۡقِلُونَ

Nena: “Idzani kuno, ndikuwerengereni zomwe Mbuye wanu wakuletsani. Musamphatikize ndi chilichonse, ndipo achitireni zabwino makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chakuopa umphawi; ife tikupatsani rizq inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zoyipa, zoonekera ndi zobisika; ndipo musaphe munthu yemwe Allah adaletsa (kumupha) kupatula ikapezeka njira yoyenereza (kumupha). Akukulangizani izi kuti muziike mu nzeru zanu.” info
التفاسير: