Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

external-link copy
61 : 28

أَفَمَن وَعَدۡنَٰهُ وَعۡدًا حَسَنٗا فَهُوَ لَٰقِيهِ كَمَن مَّتَّعۡنَٰهُ مَتَٰعَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا ثُمَّ هُوَ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ مِنَ ٱلۡمُحۡضَرِينَ

Kodi munthu yemwe tamulonjeza lonjezo labwino (kuti akalowa ku Munda wamtendere) kotero kuti iye akakumana nalo (lonjezolo), angafanane ndi yemwe tamsangalatsa ndi zosangalatsa za moyo wa pa dziko basi, kenako iye nkukhala mmodzi okaponyedwa (ku Moto) tsiku la chiweruziro (Qiyâma)? info
التفاسير: