Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

external-link copy
63 : 2

وَإِذۡ أَخَذۡنَا مِيثَٰقَكُمۡ وَرَفَعۡنَا فَوۡقَكُمُ ٱلطُّورَ خُذُواْ مَآ ءَاتَيۡنَٰكُم بِقُوَّةٖ وَٱذۡكُرُواْ مَا فِيهِ لَعَلَّكُمۡ تَتَّقُونَ

Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene tidalandira chipangano chanu (kuti mudzagwiritsa ntchito zomwe zili m’buku la Taurat), ndipo tidakweza pamwamba panu phiri (la Sinai; tidati kwa inu): “Gwirani mwamphamvu chimene takupatsani, ndipo kumbukirani zili m’menemo (pozigwiritsa ntchito. Ndiponso musazinyozere) kuti mukhale oopa Allah.” info
التفاسير: