Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
8 : 17

عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يَرۡحَمَكُمۡۚ وَإِنۡ عُدتُّمۡ عُدۡنَاۚ وَجَعَلۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ حَصِيرًا

“(Koma ngati mudzalungama mzochita zanu), Mbuye wanu adzakuchitirani chifundo; ndipo ngati mudzabwereranso (ku machitidwe anu okhota), tidzabwereranso (kukulangani). Ndipo taikonza Jahannam kukhala ndende ya osakhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 17

إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَهۡدِي لِلَّتِي هِيَ أَقۡوَمُ وَيُبَشِّرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ أَجۡرٗا كَبِيرٗا

Ndithu iyi Qur’an ikuongolera ku njira yoongoka ndi kuwasangalatsa okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti ndithu iwo adzalandira malipiro aakulu (pa tsiku la chiweruziro); info
التفاسير:

external-link copy
10 : 17

وَأَنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمٗا

Ndikutinso omwe sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro tawakonzera chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 17

وَيَدۡعُ ٱلۡإِنسَٰنُ بِٱلشَّرِّ دُعَآءَهُۥ بِٱلۡخَيۡرِۖ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ عَجُولٗا

Ndipo munthu amafulumira kupempha zoipa monga momwenso amafulumilira kupempha zabwino; ndithu munthu ngwaphuma (mzochita zake). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 17

وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ ءَايَتَيۡنِۖ فَمَحَوۡنَآ ءَايَةَ ٱلَّيۡلِ وَجَعَلۡنَآ ءَايَةَ ٱلنَّهَارِ مُبۡصِرَةٗ لِّتَبۡتَغُواْ فَضۡلٗا مِّن رَّبِّكُمۡ وَلِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ وَكُلَّ شَيۡءٖ فَصَّلۡنَٰهُ تَفۡصِيلٗا

Ndipo tapanga usiku ndi usana (mkusinthana-sinthana kwake) monga zisonyezo ziwiri (zosonyeza umodzi wa Allah ndi mphamvu Zake zoposa); ndipo tidachifafaniza chisonyezo cha usiku (kuti chisakhale ndi kuunika) ndipo chisonyezo cha usana tidachipanga kuti chikhale ndi kuunika; kuti mufunefune ubwino wochokera kwa Mbuye wanu, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka ndichiwerengero (cha miyezi ndi masiku); ndipo chinthu chilichonse (chofunika pa chipembedzo ndi za m’dziko), tachilongosola bwinobwino, mwatsatanetsatane. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 17

وَكُلَّ إِنسَٰنٍ أَلۡزَمۡنَٰهُ طَٰٓئِرَهُۥ فِي عُنُقِهِۦۖ وَنُخۡرِجُ لَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ كِتَٰبٗا يَلۡقَىٰهُ مَنشُورًا

Ndipo munthu aliyense tammangilira mkhosi mwake zochita zake; ndipo tsiku la Qiyâma tidzamtulutsira kaundula (momwe muli zochita zake), adzampeza wovundukulidwa. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 17

ٱقۡرَأۡ كِتَٰبَكَ كَفَىٰ بِنَفۡسِكَ ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكَ حَسِيبٗا

(Kudzanenedwa kwa iye:) “Werenga kaundula wako (kupyolera m’mphamvu za Allah ngakhale pa dziko lapansi siunkatha kuwerenga); mzimu wako ukwanira lero kudziwerengera.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 17

مَّنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۗ وَمَا كُنَّا مُعَذِّبِينَ حَتَّىٰ نَبۡعَثَ رَسُولٗا

Amene waongoka (potsatira njira ya choonadi) ndithu wadzipindulira yekha, ndipo amene wapotoka (ku njira ya choonadi) ndithu wadzitaya iye mwini. Ndipo msenzi wosenza machimo sadzasenza mtolo wa machimo a wina. Ndipo Ife siolanga (zolengedwa) kufikira titatumiza mtumiki (kuti azidziwitse choonadi. Zikakana ndipomwe timazilanga). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 17

وَإِذَآ أَرَدۡنَآ أَن نُّهۡلِكَ قَرۡيَةً أَمَرۡنَا مُتۡرَفِيهَا فَفَسَقُواْ فِيهَا فَحَقَّ عَلَيۡهَا ٱلۡقَوۡلُ فَدَمَّرۡنَٰهَا تَدۡمِيرٗا

Ndipo tikafuna kuononga mudzi (pamene eni mudziwo akuchita zoipa), timawalamula opeza bwino a m’menemo (kuti asiye zoipa). Koma akapitiriza kuononga kwawo m’menemo, apo ndipo liwu (la kuwaononga) limatsimikizidwa pa iwo ndipo timauononga, kuononga kwakukulu. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 17

وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِنۢ بَعۡدِ نُوحٖۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا

Ndimibadwo ingati imene tidaiononga pambuyo pa Nuh! Ndipo akukwanira Mbuye wako kudziwa bwinobwino ndi kuona bwinobwino uchimo wa akapolo Ake. (Palibe chobisika kwa Iye m’zochitachita za anthu). info
التفاسير: