Salin ng mga Kahulugan ng Marangal na Qur'an - Salin sa Wikang Chichewa ni Khalid Ibrahim Bityala

Numero ng Pahina:close

external-link copy
53 : 12

۞ وَمَآ أُبَرِّئُ نَفۡسِيٓۚ إِنَّ ٱلنَّفۡسَ لَأَمَّارَةُۢ بِٱلسُّوٓءِ إِلَّا مَا رَحِمَ رَبِّيٓۚ إِنَّ رَبِّي غَفُورٞ رَّحِيمٞ

۞ “Ndipo ine sindikuyeretsa mtima wanga. Ndithu mtima uliwonse umalamulira kwambiri ku zoipa kupatula umene Mbuye wanga wauchitira chifundo. Ndithudi, Mbuye wanga Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.” info
التفاسير:

external-link copy
54 : 12

وَقَالَ ٱلۡمَلِكُ ٱئۡتُونِي بِهِۦٓ أَسۡتَخۡلِصۡهُ لِنَفۡسِيۖ فَلَمَّا كَلَّمَهُۥ قَالَ إِنَّكَ ٱلۡيَوۡمَ لَدَيۡنَا مَكِينٌ أَمِينٞ

Choncho Mfumu idati: “Mubwere naye kwa ine kuti ine mwini ndimsankhe.” Ndipo pamene adayankhula naye, (Mfumu) idati: “Ndithu iwe lero kwa ife wakhala wolemekezeka, wokhulupirika.” info
التفاسير:

external-link copy
55 : 12

قَالَ ٱجۡعَلۡنِي عَلَىٰ خَزَآئِنِ ٱلۡأَرۡضِۖ إِنِّي حَفِيظٌ عَلِيمٞ

(Yûsuf) adati: “Ndiikeni kukhala muyang’aniri wa nkhokwe za dzinthu zam’dziko lonse. Ndithudi, ine ndine msungi wodziwa.” info
التفاسير:

external-link copy
56 : 12

وَكَذَٰلِكَ مَكَّنَّا لِيُوسُفَ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَتَبَوَّأُ مِنۡهَا حَيۡثُ يَشَآءُۚ نُصِيبُ بِرَحۡمَتِنَا مَن نَّشَآءُۖ وَلَا نُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo motero tidampatsa ulemelero Yûsuf m’dziko (la Iguputo); amakhala m’menemo paliponse pamene wafuna. Timam’bweretsera chifundo Chathu amene tamfuna, ndipo sitisokoneza malipiro a ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
57 : 12

وَلَأَجۡرُ ٱلۡأٓخِرَةِ خَيۡرٞ لِّلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ

Ndithudi malipiro a tsiku la chimaliziro ngabwino zedi kwa amene akhulupirira ndipo adali kumuopa (Allah). info
التفاسير:

external-link copy
58 : 12

وَجَآءَ إِخۡوَةُ يُوسُفَ فَدَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَعَرَفَهُمۡ وَهُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ

Ndipo adadza abale (ake) a Yûsuf (kukafuna chakudya kumeneko pamene ku Kenani kudagwa chilala chadzaoneni) ndikulowa kwa iye, ndipo (iye) adawazindikira pomwe iwo sankamzindikira. info
التفاسير:

external-link copy
59 : 12

وَلَمَّا جَهَّزَهُم بِجَهَازِهِمۡ قَالَ ٱئۡتُونِي بِأَخٖ لَّكُم مِّنۡ أَبِيكُمۡۚ أَلَا تَرَوۡنَ أَنِّيٓ أُوفِي ٱلۡكَيۡلَ وَأَنَا۠ خَيۡرُ ٱلۡمُنزِلِينَ

Ndipo pamene adawakonzera chakudya chawo, adati: “(Ngatimudzabwereranso kachiwiri) mudzabwere ndi m‘bale wanu wa kumbali ya bambo anu, kodi simuona kuti ine ndikukwaniritsa muyeso, ndipo ndine wabwino kwambiri polandira (alendo)?” info
التفاسير:

external-link copy
60 : 12

فَإِن لَّمۡ تَأۡتُونِي بِهِۦ فَلَا كَيۡلَ لَكُمۡ عِندِي وَلَا تَقۡرَبُونِ

“Koma ngati simudzandibweretsera iye, simudzakhala ndi mulingo (wachakudya) kwa ine, ndipo musadzandiyandikire.” info
التفاسير:

external-link copy
61 : 12

قَالُواْ سَنُرَٰوِدُ عَنۡهُ أَبَاهُ وَإِنَّا لَفَٰعِلُونَ

(Iwo) adati: “Tikayesetsa kuwanyengelera bambo wake za iye (kufikira akatipatse). Ndithu ife tikachita zimenezi.” info
التفاسير:

external-link copy
62 : 12

وَقَالَ لِفِتۡيَٰنِهِ ٱجۡعَلُواْ بِضَٰعَتَهُمۡ فِي رِحَالِهِمۡ لَعَلَّهُمۡ يَعۡرِفُونَهَآ إِذَا ٱنقَلَبُوٓاْ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِمۡ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ

Ndipo (Yûsuf) adati kwa anyamata ake a ntchito: “Ikani chuma chawo m’mitolo yawo kuti akachizindikire akabwerera ku mawanja awo. (Tachita izi kuti) mwina angabwelerenso (kuno).” info
التفاسير:

external-link copy
63 : 12

فَلَمَّا رَجَعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَبِيهِمۡ قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مُنِعَ مِنَّا ٱلۡكَيۡلُ فَأَرۡسِلۡ مَعَنَآ أَخَانَا نَكۡتَلۡ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ

Ndipo pamene adabwerera kwa bambo wawo, adati: “E bambo wathu! Tikamanidwa muyeso wa chakudya (pa ulendo wachiwiri pokhapokha titsagane ndi m’bale wathuyu). Choncho mtumizeni m’bale wathu pamodzi ndi ife kuti akatipimire (mlingo wokwana); ndithu ife tikamsunga.” info
التفاسير: