[490] Tanthauzo la “zabwino zambiri” apa, ndi uneneri, maphunziro, ntchito zabwino, ulemelero, kupambana pakukhala ndi omutsatira ambiri ndi zabwino zina zam’dziko lino lapansi ndi tsiku lachimaliziro, zosawerengeka zomwe sadapatsidwe aliyense pambuyo pa iye ngakhale mtsogolo mwake. Ndithu zimenezi, popanda chikaiko, ndizabwino kwambiri kuposa chuma ndi ana.
[491] Tanthauzo loti “Mbuye wako yekha umupembedze” nkuti amupembedze Allah Yekha, asachite chiphamaso, asakhale monga amene amachita mapemphero ndi cholinga choti adzionetsere kwa anthu. Ndikutinso apereke nsembe m’dzina Lake, osati azimu ndi zina zotero.
[492] Adani a Mtumiki (s.a.w) adali kukondwera kwambiri pamene ankaona kuti ana ake onse achimuna atha kumwalira, iwo ankaona kuti palibe ubwino uli onse kwa munthu pano pa dziko ngati sadapatsidwe ana achimuna ndi chuma. Pa chifukwa ichi, adali kumutcha “Abtar,” wopanda madalitso. Msura imeneyi Allah akumtonthoza Mneneriyo ndiponso akuyankha adani ake.