[417] Tanthauzo lakulemekeza dzina la Allah ndiko kukhulupilira kuti iye ndiwopatulika ku mbiri zilizonse zoipa zosamuyenera, monga kumufanizira ndizolengedwa; monga kuti anabereka kapena adaberekedwa, kapena kuti ali ndi mkazi kapenanso kuti alipo omwe amathandizana naye pa Umulungu Wake.
[418] Allah pambuyo polenga zolengedwa Zake sadangozileka kuti zisadziwe chochita, koma cholengedwa chilichonse adachilamuliratu kuti chichite zoyenera nacho, ndipo pambuyo pake adachiongolera pa chinthu chimenecho; chidadziwa, ndipo chidachita. Munthu adamusonyeza zomwe zili ndi mazunzo mkati mwake kuti adzitalikitse nazo ndiponso adamusonyeza zabwino kuti azichite.
[419] Mneneri Muhammad (s.a.w) adali munthu monga anthu ena ndipo adali ndi mbiri zonga anthu adalinazo, monga: kukonda ndi kusakonda, kuiwala ndi kukumbukira. Padapezeka kuti nthawi ina adaiwala ndi kupemphera maraka atatu m’Swala ya maraka anayi. Pachifukwa ichi pa nthawi yovumbulutsidwa Qur’an ndi Jibril, adali akubwereza bwereza mawu ovumbulutsidwawo kuopa kuti angaiwale. Choncho, apa Allah akumuletsa kuti asadzivutitse kumabwerezabwereza mawuwo pamene akuvumbulutsidwa ndipo adamupatsa lonjezo nthawi yomweyo kuti sadzaiwala. Ndipo adakwaniritsa lonjezo Lake. Mtumiki (s.a.w) adali kumtsikira ma surah aataliatali ndipo amatha kuwawerenga (molakatula) popanda kuonjezera kanthu kapena kuchepetsa, ngakhale kuti iye sadali kudziwa kuwerenga ndi kulemba. Kuwerenga kwake kudali kwakungolakatula pa mtima.
[420] Tanthauzo la ‘kufewetsa’ ndiko kuti Shariya ya Chisilamu (malamulo) siili yovuta kuyikwaniritsa monga momwe adalili malamulo a zipembedzo zoyamba. Ndipo ndi malamulo othandiza anthu onse, nthawi zonse ndi pamalo paliponse.
[421] Tanthauzo la apa sikuti Mtumiki (s.a.w) alalikire pokhapokha waona kuti ulalikiwo uthandiza ayi, koma alalikire ndithu kaya kulalikirako kuthandiza kapena ayi, monga momwe zalongosolera Ayah zotsatirazi. Kuyankhula kotere, Arabu amakutcha “iktifa.”