పవిత్ర ఖురాన్ యొక్క భావార్థాల అనువాదం - చిచియో అనువాదం - ఖాలిద్ ఇబ్రాహీమ్ బైతాలా

పేజీ నెంబరు:close

external-link copy
6 : 39

خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ ثُمَّ جَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ ثَمَٰنِيَةَ أَزۡوَٰجٖۚ يَخۡلُقُكُمۡ فِي بُطُونِ أُمَّهَٰتِكُمۡ خَلۡقٗا مِّنۢ بَعۡدِ خَلۡقٖ فِي ظُلُمَٰتٖ ثَلَٰثٖۚ ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡ لَهُ ٱلۡمُلۡكُۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ فَأَنَّىٰ تُصۡرَفُونَ

Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah?) info
التفاسير:

external-link copy
7 : 39

إِن تَكۡفُرُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَنِيٌّ عَنكُمۡۖ وَلَا يَرۡضَىٰ لِعِبَادِهِ ٱلۡكُفۡرَۖ وَإِن تَشۡكُرُواْ يَرۡضَهُ لَكُمۡۗ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۚ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّكُم مَّرۡجِعُكُمۡ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَۚ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ

Ngati mukana ndithu Allah Ngodzikwaniritsa sasaukira kwa inu (chikhulupiliro chanu ndi kuthokoza kwanu); koma sakonda kukanira kwa anthu Ake. Ngati mumthokoza (pa mtendere Wake umene uli pa inu) akuyanja kuthokoza kwanuko. Ndipo mzimu wochimwa sungasenze machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu nkwa Mbuye wanu, ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita. Ndithu Iye Ngodziwa (zinsinsi) za m’mitima. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 39

۞ وَإِذَا مَسَّ ٱلۡإِنسَٰنَ ضُرّٞ دَعَا رَبَّهُۥ مُنِيبًا إِلَيۡهِ ثُمَّ إِذَا خَوَّلَهُۥ نِعۡمَةٗ مِّنۡهُ نَسِيَ مَا كَانَ يَدۡعُوٓاْ إِلَيۡهِ مِن قَبۡلُ وَجَعَلَ لِلَّهِ أَندَادٗا لِّيُضِلَّ عَن سَبِيلِهِۦۚ قُلۡ تَمَتَّعۡ بِكُفۡرِكَ قَلِيلًا إِنَّكَ مِنۡ أَصۡحَٰبِ ٱلنَّارِ

Ndipo masautso akampeza munthu, amapempha Mbuye wake ndi kutembenukira kwa Iye (pomwe chikhalirecho adali kumnyoza). Kenako (Mbuye wake) akampatsa mtendere wochokera kwa Iye (waukulu), amaiwala (masautso aja) omwe adali kumpempha Allah kuti amchotsere asadampatse mtenderewo, ndipo kenako ndikumpangira Allah milungu inzake kuti asokeretse ku njira Yake. Nena (iwe Mtumiki kwa yemwe ali ndi chikhalidwe chotere): “Sangalala ndi kukanira kwako (mtendere wa Allah) kwa nthawi yochepa. Ndithu iwe ndi mmodzi wa anthu aku Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 39

أَمَّنۡ هُوَ قَٰنِتٌ ءَانَآءَ ٱلَّيۡلِ سَاجِدٗا وَقَآئِمٗا يَحۡذَرُ ٱلۡأٓخِرَةَ وَيَرۡجُواْ رَحۡمَةَ رَبِّهِۦۗ قُلۡ هَلۡ يَسۡتَوِي ٱلَّذِينَ يَعۡلَمُونَ وَٱلَّذِينَ لَا يَعۡلَمُونَۗ إِنَّمَا يَتَذَكَّرُ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ

Kodi yemwe akudzichepetsa (kwa Allah ndi kumpembedza) pakati pa usiku uku akugwetsa nkhope pansi ndi kuimilira, kuopa tsiku la chimaliziro ndi kuyembekezera chifundo cha Mbuye wake, (kodi angafanane ndi yemwe amapempha Allah akakhala pa mavuto pokha, akakhala pa mtendere ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki {s.a.w}): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu ndi eni nzeru amene amalingalira. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 39

قُلۡ يَٰعِبَادِ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّقُواْ رَبَّكُمۡۚ لِلَّذِينَ أَحۡسَنُواْ فِي هَٰذِهِ ٱلدُّنۡيَا حَسَنَةٞۗ وَأَرۡضُ ٱللَّهِ وَٰسِعَةٌۗ إِنَّمَا يُوَفَّى ٱلصَّٰبِرُونَ أَجۡرَهُم بِغَيۡرِ حِسَابٖ

Nena (kwa iwo mau Anga akuti): “E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Muopeni Mbuye wanu. Ndithu amene achita zabwino zotsatira zake nzabwino padziko lapansi, ndipo dziko la Allah ndilophanuka. (Pirirani chifukwa chosiya midzi yanu ndi abale). Ndithu opirira adzalipidwa malipiro awo mokwana mopanda mulingo.” info
التفاسير: