పవిత్ర ఖురాన్ యొక్క భావార్థాల అనువాదం - చిచియో అనువాదం - ఖాలిద్ ఇబ్రాహీమ్ బైతాలా

పేజీ నెంబరు:close

external-link copy
109 : 11

فَلَا تَكُ فِي مِرۡيَةٖ مِّمَّا يَعۡبُدُ هَٰٓؤُلَآءِۚ مَا يَعۡبُدُونَ إِلَّا كَمَا يَعۡبُدُ ءَابَآؤُهُم مِّن قَبۡلُۚ وَإِنَّا لَمُوَفُّوهُمۡ نَصِيبَهُمۡ غَيۡرَ مَنقُوصٖ

Choncho, usakhale ndi chipeneko pa zimene awa akuzipembedza (kuti ndimilungu yabodza). Sapembedza koma momwe amapembedzera makolo awo kale. Ndipo ndithu Ife tiwapatsa gawo lawo (la chilango) mokwanira popanda kuchepetsa. info
التفاسير:

external-link copy
110 : 11

وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ فَٱخۡتُلِفَ فِيهِۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ لَقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّهُمۡ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُ مُرِيبٖ

Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo. info
التفاسير:

external-link copy
111 : 11

وَإِنَّ كُلّٗا لَّمَّا لَيُوَفِّيَنَّهُمۡ رَبُّكَ أَعۡمَٰلَهُمۡۚ إِنَّهُۥ بِمَا يَعۡمَلُونَ خَبِيرٞ

Ndipo ndithu Mbuye wako adzawapatsa onsewo mphoto ya zochita zawo mokwanira. Ndithu Iye Ngodziwa (zonse) zimene akuchita. info
التفاسير:

external-link copy
112 : 11

فَٱسۡتَقِمۡ كَمَآ أُمِرۡتَ وَمَن تَابَ مَعَكَ وَلَا تَطۡغَوۡاْۚ إِنَّهُۥ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ

Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita.[226] info

[226] Apa akutanthauza kuti ngati chikhalidwe cha mibadwo yakale chidali chonchi, mibadwo yomwe adaitumizira buku lake, natsutsana ndi bukuli, ena a iwo nalitaya kutali, iweyo pitiriza ndi Asilamu omwe uli nawo kugwira njira yolungama monga momwe Allah wakulamulira. Usapyole malire ponyozera chimene chili choyenera iwe kuchichita, kapena kudzikakamiza chimene sungathe kuchichita. Allah tu akudziwa zonse zomwe muchita ndipo adzakulipirani.

التفاسير:

external-link copy
113 : 11

وَلَا تَرۡكَنُوٓاْ إِلَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ فَتَمَسَّكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِنۡ أَوۡلِيَآءَ ثُمَّ لَا تُنصَرُونَ

Ndipo musapendekere kwa amene sali olungama kuopa kuti chilango cha Moto chingakukhudzeni; ndipo simudzakhala ndi atetezi kwa Allah, ndipo potero simudzathandizidwa (chilichonse). info
التفاسير:

external-link copy
114 : 11

وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ طَرَفَيِ ٱلنَّهَارِ وَزُلَفٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِۚ إِنَّ ٱلۡحَسَنَٰتِ يُذۡهِبۡنَ ٱلسَّيِّـَٔاتِۚ ذَٰلِكَ ذِكۡرَىٰ لِلذَّٰكِرِينَ

Ndipo pemphera Swala nsonga ziwiri za usana ndi nthawi za usiku zomwe zili pafupi ndi usana. Ndithu zabwino zimachotsa zoipa. Ichi ndi chikumbutso kwa okumbukira. info
التفاسير:

external-link copy
115 : 11

وَٱصۡبِرۡ فَإِنَّ ٱللَّهَ لَا يُضِيعُ أَجۡرَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndipo pirira (E iwe Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo a Mbuye wako)! Ndithu Allah sataya malipiro a ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
116 : 11

فَلَوۡلَا كَانَ مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِن قَبۡلِكُمۡ أُوْلُواْ بَقِيَّةٖ يَنۡهَوۡنَ عَنِ ٱلۡفَسَادِ فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا قَلِيلٗا مِّمَّنۡ أَنجَيۡنَا مِنۡهُمۡۗ وَٱتَّبَعَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مَآ أُتۡرِفُواْ فِيهِ وَكَانُواْ مُجۡرِمِينَ

Kodi bwanji sadakhalepo, mu mibadwo ya anthu akale, eni nzeru (omvera akalangizidwa), oletsa kuononga pa dziko kupatula ochepa amene tidawapulumutsa mwa iwo? Ndipo amene adadzichitira okha zoipa adatsata zomwe adasangalatsidwa nazo, choncho, adali ochita zoipa. info
التفاسير:

external-link copy
117 : 11

وَمَا كَانَ رَبُّكَ لِيُهۡلِكَ ٱلۡقُرَىٰ بِظُلۡمٖ وَأَهۡلُهَا مُصۡلِحُونَ

Ndipo Mbuye wako sali woononga midzi mopanda chilungamo pomwe eni ake (midziyo) ali ochita zabwino. info
التفاسير: