அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா

பக்க எண்:close

external-link copy
91 : 5

إِنَّمَا يُرِيدُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَن يُوقِعَ بَيۡنَكُمُ ٱلۡعَدَٰوَةَ وَٱلۡبَغۡضَآءَ فِي ٱلۡخَمۡرِ وَٱلۡمَيۡسِرِ وَيَصُدَّكُمۡ عَن ذِكۡرِ ٱللَّهِ وَعَنِ ٱلصَّلَوٰةِۖ فَهَلۡ أَنتُم مُّنتَهُونَ

Ndithudi, satana akufuna kudzetsa chidani ndi kusakondana pakati panu kudzera m’mowa ndi njuga, ndikuti akutsekerezeni kukumbukira Allah ndi kupemphera Swala. Kodi inu simusiya? info
التفاسير:

external-link copy
92 : 5

وَأَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَ وَٱحۡذَرُواْۚ فَإِن تَوَلَّيۡتُمۡ فَٱعۡلَمُوٓاْ أَنَّمَا عَلَىٰ رَسُولِنَا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ

Mverani Allah, ndipo mverani Mtumiki ndipo chenjerani (musanyoze malamulo a Allah). Ngati munyoza, dziwani kuti udindo wa Mtumiki Wathu ndikufikitsa uthenga woonekera basi. info
التفاسير:

external-link copy
93 : 5

لَيۡسَ عَلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جُنَاحٞ فِيمَا طَعِمُوٓاْ إِذَا مَا ٱتَّقَواْ وَّءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ ثُمَّ ٱتَّقَواْ وَّءَامَنُواْ ثُمَّ ٱتَّقَواْ وَّأَحۡسَنُواْۚ وَٱللَّهُ يُحِبُّ ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Palibe tchimo kwa amene akhulupirira ndi kuchita zabwino pazomwe adadya (zisadaletsedwe) ngati akupitiriza kuopa ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; kenako nkuopanso (ataletsedwa zina) ndikukhulupirira; (atalamulidwa zinanso) nkuopanso ndikuchita zabwino. Ndipo Allah, amakonda ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
94 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَيَبۡلُوَنَّكُمُ ٱللَّهُ بِشَيۡءٖ مِّنَ ٱلصَّيۡدِ تَنَالُهُۥٓ أَيۡدِيكُمۡ وَرِمَاحُكُمۡ لِيَعۡلَمَ ٱللَّهُ مَن يَخَافُهُۥ بِٱلۡغَيۡبِۚ فَمَنِ ٱعۡتَدَىٰ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَلَهُۥ عَذَابٌ أَلِيمٞ

E inu amene mwakhulupirira! Ndithu Allah akuyesani ndi nyama zina zozichita ulenje, zomwe manja anu ndi mikondo yanu ingazifikire, kuti Allah amuwonetsere poyera amene akumuopa mwanseri. Ndipo amene alumphe malire (posaka nyamayo ndi kupha) pambuyo pa zomwe mwauzidwazo, adzapeza chilango chopweteka. info
التفاسير:

external-link copy
95 : 5

يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَقۡتُلُواْ ٱلصَّيۡدَ وَأَنتُمۡ حُرُمٞۚ وَمَن قَتَلَهُۥ مِنكُم مُّتَعَمِّدٗا فَجَزَآءٞ مِّثۡلُ مَا قَتَلَ مِنَ ٱلنَّعَمِ يَحۡكُمُ بِهِۦ ذَوَا عَدۡلٖ مِّنكُمۡ هَدۡيَۢا بَٰلِغَ ٱلۡكَعۡبَةِ أَوۡ كَفَّٰرَةٞ طَعَامُ مَسَٰكِينَ أَوۡ عَدۡلُ ذَٰلِكَ صِيَامٗا لِّيَذُوقَ وَبَالَ أَمۡرِهِۦۗ عَفَا ٱللَّهُ عَمَّا سَلَفَۚ وَمَنۡ عَادَ فَيَنتَقِمُ ٱللَّهُ مِنۡهُۚ وَٱللَّهُ عَزِيزٞ ذُو ٱنتِقَامٍ

E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa info
التفاسير: