அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா

Ad-Dukhân

external-link copy
1 : 44

حمٓ

Hâ-Mîm. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 44

وَٱلۡكِتَٰبِ ٱلۡمُبِينِ

Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 44

إِنَّآ أَنزَلۡنَٰهُ فِي لَيۡلَةٖ مُّبَٰرَكَةٍۚ إِنَّا كُنَّا مُنذِرِينَ

Ndithu tidaivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wodala. Ife ndithu Ndiachenjezi. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 44

فِيهَا يُفۡرَقُ كُلُّ أَمۡرٍ حَكِيمٍ

Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 44

أَمۡرٗا مِّنۡ عِندِنَآۚ إِنَّا كُنَّا مُرۡسِلِينَ

Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu). info
التفاسير:

external-link copy
6 : 44

رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

(Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 44

رَبِّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَآۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ

Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli otsimikiza. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 44

لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحۡيِۦ وَيُمِيتُۖ رَبُّكُمۡ وَرَبُّ ءَابَآئِكُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ

Palibe wopembedzedwa moona koma Iye basi. Amapereka moyo ndikupereka imfa, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu oyamba. info
التفاسير:

external-link copy
9 : 44

بَلۡ هُمۡ فِي شَكّٖ يَلۡعَبُونَ

Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa). info
التفاسير:

external-link copy
10 : 44

فَٱرۡتَقِبۡ يَوۡمَ تَأۡتِي ٱلسَّمَآءُ بِدُخَانٖ مُّبِينٖ

Basi, yembekezera tsiku limene thambo lidzadze ndi utsi woonekera (konsekonse). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 44

يَغۡشَى ٱلنَّاسَۖ هَٰذَا عَذَابٌ أَلِيمٞ

Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa. info
التفاسير:

external-link copy
12 : 44

رَّبَّنَا ٱكۡشِفۡ عَنَّا ٱلۡعَذَابَ إِنَّا مُؤۡمِنُونَ

E Mbuye wathu! Tichotsereni chilangochi, ndithu ife tikhulupirira.” info
التفاسير:

external-link copy
13 : 44

أَنَّىٰ لَهُمُ ٱلذِّكۡرَىٰ وَقَدۡ جَآءَهُمۡ رَسُولٞ مُّبِينٞ

(Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera. info
التفاسير:

external-link copy
14 : 44

ثُمَّ تَوَلَّوۡاْ عَنۡهُ وَقَالُواْ مُعَلَّمٞ مَّجۡنُونٌ

Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.” info
التفاسير:

external-link copy
15 : 44

إِنَّا كَاشِفُواْ ٱلۡعَذَابِ قَلِيلًاۚ إِنَّكُمۡ عَآئِدُونَ

Ndithu Ife tichotsa chilangocho pang’ono (koma) inu mubwerezanso (machimo anu). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 44

يَوۡمَ نَبۡطِشُ ٱلۡبَطۡشَةَ ٱلۡكُبۡرَىٰٓ إِنَّا مُنتَقِمُونَ

(Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 44

۞ وَلَقَدۡ فَتَنَّا قَبۡلَهُمۡ قَوۡمَ فِرۡعَوۡنَ وَجَآءَهُمۡ رَسُولٞ كَرِيمٌ

Ndipo ndithu iwo asadadze, tidawayesa anthu a Farawo. Ndiponso adawadzera mtumiki wolemekezeka, info
التفاسير:

external-link copy
18 : 44

أَنۡ أَدُّوٓاْ إِلَيَّ عِبَادَ ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُمۡ رَسُولٌ أَمِينٞ

Kuti: “Ndipatseni akapolo a Allah. Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki wokhulupirika.” info
التفاسير: