[332] M’ndime iyi Allah akutidziwitsa kuti akudziwa zonse zimene zikulowa m’nthaka monga madzi, mitembo ndi zina zotero. Ndipo akudziwanso zimene zikutuluka m’menemo - monga mmera tizirombo, miyala yamtengo wapatali ndi madzi. Ndi zomwe zikutsika kumwamba monga mvula, matalala, mphenzi, madalitso, angelo Ake ndi mabuku Ake. Ndipo akudziwanso zimene zikukwera kumwamba - monga ntchito za akapolo Ake ndi zina zotero.