அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா

Al-’Ankabût

external-link copy
1 : 29

الٓمٓ

Alif-Lâm-Mîm. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 29

أَحَسِبَ ٱلنَّاسُ أَن يُتۡرَكُوٓاْ أَن يَقُولُوٓاْ ءَامَنَّا وَهُمۡ لَا يُفۡتَنُونَ

Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupirira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu ndi masautso osiyanasiyana pa matupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 29

وَلَقَدۡ فَتَنَّا ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ فَلَيَعۡلَمَنَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ صَدَقُواْ وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱلۡكَٰذِبِينَ

Ndipo ndithu tidawayesa amene adalipo patsogolo pawo. Ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zoona, ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zabodza. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 29

أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن يَسۡبِقُونَاۚ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ

Kodi amene akuchita zoipa akuganiza kuti atipambana (kotero kuti sitingawalange)? Ndichiweruzo choipa chimene akuweruzacho. info
التفاسير:

external-link copy
5 : 29

مَن كَانَ يَرۡجُواْ لِقَآءَ ٱللَّهِ فَإِنَّ أَجَلَ ٱللَّهِ لَأٓتٖۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ

Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo).[299] info

[299] Tanthauzo la ndimeyi nkuti amene akuyembekezera kuti akalandire malipiro abwino kwa Allah, apirire pa moyo wa pa dziko lapansi polimbika kumvera Allah mpaka adzakumane ndi Allah. Ndithudi, kukumana ndi Allah kuli pafupi.

التفاسير:

external-link copy
6 : 29

وَمَن جَٰهَدَ فَإِنَّمَا يُجَٰهِدُ لِنَفۡسِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَغَنِيٌّ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ

Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake. info
التفاسير: