அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா

பக்க எண்:close

external-link copy
67 : 17

وَإِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فِي ٱلۡبَحۡرِ ضَلَّ مَن تَدۡعُونَ إِلَّآ إِيَّاهُۖ فَلَمَّا نَجَّىٰكُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ أَعۡرَضۡتُمۡۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ كَفُورًا

Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika.) info
التفاسير:

external-link copy
68 : 17

أَفَأَمِنتُمۡ أَن يَخۡسِفَ بِكُمۡ جَانِبَ ٱلۡبَرِّ أَوۡ يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗا ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ وَكِيلًا

Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)? info
التفاسير:

external-link copy
69 : 17

أَمۡ أَمِنتُمۡ أَن يُعِيدَكُمۡ فِيهِ تَارَةً أُخۡرَىٰ فَيُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ قَاصِفٗا مِّنَ ٱلرِّيحِ فَيُغۡرِقَكُم بِمَا كَفَرۡتُمۡ ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ عَلَيۡنَا بِهِۦ تَبِيعٗا

Kapena mwadziika pachitetezo kuti (Allah) sadzakubwezeraninso m’nyanjamo kachiwiri ndipo nkudzakutumizirani chimphepo chaukali ndikukumizani chifukwa cha kusakhulupirira (ndi kusathokoza kwanu,) kenako inu nkusapeza wokutetezani kwa Ife? info
التفاسير:

external-link copy
70 : 17

۞ وَلَقَدۡ كَرَّمۡنَا بَنِيٓ ءَادَمَ وَحَمَلۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّمَّنۡ خَلَقۡنَا تَفۡضِيلٗا

Ndipo ndithu tawalemekeza ana a Adam; ndipo tawapatsa zokwera pa ntunda ndi pa nyanja; tawapatsa zopatsa zabwino kwambiri; ndipo tawapatsa ulemelero kuposa zambiri m’zomwe tidalenga; ulemelero waukulu kwabasi. info
التفاسير:

external-link copy
71 : 17

يَوۡمَ نَدۡعُواْ كُلَّ أُنَاسِۭ بِإِمَٰمِهِمۡۖ فَمَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَقۡرَءُونَ كِتَٰبَهُمۡ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلٗا

(Akumbutse za) tsiku lomwe tidzaitana anthu onse m’dzina la mneneri wawo; choncho, amene adzapatsidwe akaundula awo ndi dzanja lamanja iwo adzawerenga akaundula awowo (mwachisangalalo), ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pa (kachinthu kakang’ono monga) kaulusi ka mkati mwa njere ya kanjeza. info
التفاسير:

external-link copy
72 : 17

وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِۦٓ أَعۡمَىٰ فَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلٗا

Ndipo amene ali wakhungu pano (pa dziko lapansi posapenya zizindikiro) adzakhalanso wakhungu pa tsiku la chimaliziro, ndipo adzakhala wosokera kwambiri njira (kumeneko). info
التفاسير:

external-link copy
73 : 17

وَإِن كَادُواْ لَيَفۡتِنُونَكَ عَنِ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ لِتَفۡتَرِيَ عَلَيۡنَا غَيۡرَهُۥۖ وَإِذٗا لَّٱتَّخَذُوكَ خَلِيلٗا

Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo). info
التفاسير:

external-link copy
74 : 17

وَلَوۡلَآ أَن ثَبَّتۡنَٰكَ لَقَدۡ كِدتَّ تَرۡكَنُ إِلَيۡهِمۡ شَيۡـٔٗا قَلِيلًا

Ndipo tikadapanda kukulimbikitsa, ukadapendekera kwa iwo, kupendekera kwa pang’ono. info
التفاسير:

external-link copy
75 : 17

إِذٗا لَّأَذَقۡنَٰكَ ضِعۡفَ ٱلۡحَيَوٰةِ وَضِعۡفَ ٱلۡمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيۡنَا نَصِيرٗا

Tero ndithu tikadakulawitsa chilango chachikulu cha moyo (wa pa dziko lapansi) ndi chilango chachikulu utafa; kenako siukadapeza mthandizi wokupulumutsa kwa Ife. info
التفاسير: