[219] Mawu oti “Riziki lake lili kwa Allah’’ nkuti Allah wapatsa chilichonse mphamvu zofunira riziki lake (zoyendetsa moyo wake). Ndimeyi siitanthauza kuti munthu angokhala popanda kugwira ntchito nayembekezera kuti riziki lichokera kumwamba. Koma munthu agwire ntchito molimbikira kuti apeze chuma cha Allah. Zotere nzimene Qur’an ikutilangiza.
[220] Kunena kwakuti thambo ndi nthaka zidalengedwa m’masiku asanu ndi limodzi, amene akudziwa za masiku asanu ndi limodziwo momwe adalili ndi Allah yekha. Ndiponso mpandowo sitikudziwa tsatanetsatane wake. Chimene chilipo kwa ife nkukhulupilira basi.
[221] Ophatikiza Allah ndi zina zake adali kupereka maganizo kwa Mtumiki akuti ampemphe Allah kuti adzetse milumilu ya chuma kapena amutumizire angelo kuti aziyenda naye limodzi. Ndipo adalinso kumaichitira Qur’an chibwana Mtumiki akawawerengera. Potero Mtumiki (s.a.w) adali kubanika mu mtima mwake akafuna kufikitsa uthenga kwa iwo chifukwa chakuopa kutsutsidwa ndi kumchitira chibwana.