د قرآن کریم د معناګانو ژباړه - چیچوایي ژباړه - خالد ابراهیم بتیالا

AL-Muddaththir

external-link copy
1 : 74

يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمُدَّثِّرُ

E iwe wadziphimba (nsalu)! info
التفاسير:

external-link copy
2 : 74

قُمۡ فَأَنذِرۡ

Imilira ndipo uwachenjeze (anthu za chilango cha Allah). info
التفاسير:

external-link copy
3 : 74

وَرَبَّكَ فَكَبِّرۡ

Ndipo Mbuye wako (Yekha) umkulitse (pomulemekeza). info
التفاسير:

external-link copy
4 : 74

وَثِيَابَكَ فَطَهِّرۡ

Ndipo nsalu zako uziyeretse (ndi madzi ku uve). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 74

وَٱلرُّجۡزَ فَٱهۡجُرۡ

Ndiponso zoipa (monga mafano ndi zina zonse ) zipewe. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 74

وَلَا تَمۡنُن تَسۡتَكۡثِرُ

Usapatse (anthu) ncholinga choti ulandire zambiri. info
التفاسير:

external-link copy
7 : 74

وَلِرَبِّكَ فَٱصۡبِرۡ

Chifukwa cha Mbuye wako, pirira (ku malamulo Ake poleka zomwe waletsa ndi kuchita zimene walamula). info
التفاسير:

external-link copy
8 : 74

فَإِذَا نُقِرَ فِي ٱلنَّاقُورِ

Ndipo likadzaimbidwa lipenga, info
التفاسير:

external-link copy
9 : 74

فَذَٰلِكَ يَوۡمَئِذٖ يَوۡمٌ عَسِيرٌ

Tsiku limenelo lidzakhala tsiku lovuta. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 74

عَلَى ٱلۡكَٰفِرِينَ غَيۡرُ يَسِيرٖ

Kwa osakhulupirira, silidzakhala lofewa. info
التفاسير:

external-link copy
11 : 74

ذَرۡنِي وَمَنۡ خَلَقۡتُ وَحِيدٗا

Ndisiye ndiamene ndidamlenga Ndekha, info
التفاسير:

external-link copy
12 : 74

وَجَعَلۡتُ لَهُۥ مَالٗا مَّمۡدُودٗا

Ndipo ndampatsa chuma chambiri. info
التفاسير:

external-link copy
13 : 74

وَبَنِينَ شُهُودٗا

Ndi ana okhala nawo (paliponse). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 74

وَمَهَّدتُّ لَهُۥ تَمۡهِيدٗا

Ndipo ndamkonzera (ulemelero), kumkonzera (kwabwino). info
التفاسير:

external-link copy
15 : 74

ثُمَّ يَطۡمَعُ أَنۡ أَزِيدَ

Kenako ali ndi dyera kuti ndimuonjezere (zina popanda kuthokoza). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 74

كَلَّآۖ إِنَّهُۥ كَانَ لِأٓيَٰتِنَا عَنِيدٗا

Koma sichoncho! Ndithu iye adali kutsutsa zizindikiro Zathu. info
التفاسير:

external-link copy
17 : 74

سَأُرۡهِقُهُۥ صَعُودًا

Ndidzamkakamiza kuchilango chovuta; (kukwera phiri la ku Moto limene sakatha kulikwera). info
التفاسير:

external-link copy
18 : 74

إِنَّهُۥ فَكَّرَ وَقَدَّرَ

Iye adalingalira (mu mtima mwake) ndi kukonza bwino (chonena chonyoza Qur’an). info
التفاسير:

external-link copy
19 : 74

فَقُتِلَ كَيۡفَ قَدَّرَ

Choncho waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)! info
التفاسير:

external-link copy
20 : 74

ثُمَّ قُتِلَ كَيۡفَ قَدَّرَ

Ndiponso waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)! info
التفاسير:

external-link copy
21 : 74

ثُمَّ نَظَرَ

Kenako adayang’anayang’ana (nkhope za anthu). info
التفاسير:

external-link copy
22 : 74

ثُمَّ عَبَسَ وَبَسَرَ

Kenakonso adachita tsinya ndikukwinya nkhope (kwambiri ndi mkwiyo). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 74

ثُمَّ أَدۡبَرَ وَٱسۡتَكۡبَرَ

Kenakonso adanyoza choonadi ndi kudzikweza (posachivomereza), info
التفاسير:

external-link copy
24 : 74

فَقَالَ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا سِحۡرٞ يُؤۡثَرُ

Adati: “Sichina ichi (Qur’an) koma ndi matsenga amene adalandiridwa (kuchokera kwa amatsenga akale), info
التفاسير:

external-link copy
25 : 74

إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا قَوۡلُ ٱلۡبَشَرِ

Sichina ichi koma ndi mawu a anthu!” info
التفاسير:

external-link copy
26 : 74

سَأُصۡلِيهِ سَقَرَ

Posachedwa ndimlowetsa ku ‘Saqara.’ info
التفاسير:

external-link copy
27 : 74

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا سَقَرُ

Nanga ndi chiyani chingakudziwitse za ‘Saqara?’ info
التفاسير:

external-link copy
28 : 74

لَا تُبۡقِي وَلَا تَذَرُ

(Ndi moto umene) siusiya (mnofu) ndiponso siusiya (fupa), info
التفاسير:

external-link copy
29 : 74

لَوَّاحَةٞ لِّلۡبَشَرِ

Wopsereza ndi kudetsa khungu. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 74

عَلَيۡهَا تِسۡعَةَ عَشَرَ

Kumeneko kuli khumi ndi asanu ndi anayi (alonda oyang’anira Motowo.) info
التفاسير:

external-link copy
31 : 74

وَمَا جَعَلۡنَآ أَصۡحَٰبَ ٱلنَّارِ إِلَّا مَلَٰٓئِكَةٗۖ وَمَا جَعَلۡنَا عِدَّتَهُمۡ إِلَّا فِتۡنَةٗ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ لِيَسۡتَيۡقِنَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ وَيَزۡدَادَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِيمَٰنٗا وَلَا يَرۡتَابَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَلِيَقُولَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ وَٱلۡكَٰفِرُونَ مَاذَآ أَرَادَ ٱللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِي مَن يَشَآءُۚ وَمَا يَعۡلَمُ جُنُودَ رَبِّكَ إِلَّا هُوَۚ وَمَا هِيَ إِلَّا ذِكۡرَىٰ لِلۡبَشَرِ

Ndipo sitidaike oyang’anira ku Moto (kukhala anthu) koma angelo; ndipo sitidaike chiwerengero chawo koma ndimayesero kwa amene sadakhulupirire, kuti atsimikize amene adapatsidwa mabuku (zimene Qur’an ikunena za chiwerengero cha angelo a ku Moto) ndiponso kuti chionjezeke chikhulupiliro kwa amene akhulupirira, ndikuti asapeneke amene adapatsidwa mabuku pamodzi ndi okhulupirira. Ndiponso kuti amene m’mitima mwawo muli matenda (matenda achinyengo) komanso osakhulupirira anene: “Kodi Allah akulinganji pa fanizo limeneli?” Momwemo Allah akumulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo akumuongola amene wamfuna ndipo palibe amene angadziwe magulu a nkhondo a Mbuye wako kupatula Iye mwini. (Kutchula moto ndi zam’kati mwake) sichina koma ndichenjezo kwa anthu. info
التفاسير:

external-link copy
32 : 74

كَلَّا وَٱلۡقَمَرِ

Sichoncho; ndikulumbilira mwezi, info
التفاسير:

external-link copy
33 : 74

وَٱلَّيۡلِ إِذۡ أَدۡبَرَ

Ndi usiku pamene ukuchoka, info
التفاسير:

external-link copy
34 : 74

وَٱلصُّبۡحِ إِذَآ أَسۡفَرَ

Ndi m’bandakucha pamene kukuyera. info
التفاسير:

external-link copy
35 : 74

إِنَّهَا لَإِحۡدَى ٱلۡكُبَرِ

Ndithu uwo, (moto wa Jahannam) ndi chimodzi mwa malodza akulu, info
التفاسير:

external-link copy
36 : 74

نَذِيرٗا لِّلۡبَشَرِ

Ndi chenjezo kwa anthu, info
التفاسير:

external-link copy
37 : 74

لِمَن شَآءَ مِنكُمۡ أَن يَتَقَدَّمَ أَوۡ يَتَأَخَّرَ

Kwa yemwe wafuna mwa inu kutsogola (pochita zabwino zokamthandiza tsiku louka kwa akufa) kapena kutsalira (ndi za m’dziko). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 74

كُلُّ نَفۡسِۭ بِمَا كَسَبَتۡ رَهِينَةٌ

Mzimu uliwonse ukakhala chikole ndi zimene udachita. info
التفاسير:

external-link copy
39 : 74

إِلَّآ أَصۡحَٰبَ ٱلۡيَمِينِ

Kupatula akudzanja lamanja (Asilamu amene adadzimasula okha potembenukira kwa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
40 : 74

فِي جَنَّٰتٖ يَتَسَآءَلُونَ

(Iwo) adzakhala m’minda (yosasimbika kukongola kwake) akufunsana wina ndi mnzake, info
التفاسير:

external-link copy
41 : 74

عَنِ ٱلۡمُجۡرِمِينَ

Za anthu oipa, info
التفاسير:

external-link copy
42 : 74

مَا سَلَكَكُمۡ فِي سَقَرَ

(Kuti): “Nchiyani chakulowetsani ku Moto?” info
التفاسير:

external-link copy
43 : 74

قَالُواْ لَمۡ نَكُ مِنَ ٱلۡمُصَلِّينَ

Adzanena: “Sitidali m’gulu la omwe adali kupemphera (Swala). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 74

وَلَمۡ نَكُ نُطۡعِمُ ٱلۡمِسۡكِينَ

Ndiponso sitidali kuwadyetsa masikini. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 74

وَكُنَّا نَخُوضُ مَعَ ٱلۡخَآئِضِينَ

Koma tinkangomira (m’zachabe ndi zabodza) pamodzi ndi omira (m’menemo). info
التفاسير:

external-link copy
46 : 74

وَكُنَّا نُكَذِّبُ بِيَوۡمِ ٱلدِّينِ

Ndiponso tidali kutsutsa za tsiku la malipiro. info
التفاسير:

external-link copy
47 : 74

حَتَّىٰٓ أَتَىٰنَا ٱلۡيَقِينُ

Mpaka imfa idatifika.” info
التفاسير:

external-link copy
48 : 74

فَمَا تَنفَعُهُمۡ شَفَٰعَةُ ٱلشَّٰفِعِينَ

Choncho siwudzawathandiza uwomboli wa awomboli. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 74

فَمَا لَهُمۡ عَنِ ٱلتَّذۡكِرَةِ مُعۡرِضِينَ

Kodi ali ndi chiyani iwo pakuti azinyozera chenjezoli (limene lili Qur’an?) info
التفاسير:

external-link copy
50 : 74

كَأَنَّهُمۡ حُمُرٞ مُّسۡتَنفِرَةٞ

(Akuyenda mothamanga kuti asamve chenjezoli) ngati kuti iwo ndi mbidzi zothawa, info
التفاسير:

external-link copy
51 : 74

فَرَّتۡ مِن قَسۡوَرَةِۭ

(Zimene) zikuthawa mkango. info
التفاسير:

external-link copy
52 : 74

بَلۡ يُرِيدُ كُلُّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُمۡ أَن يُؤۡتَىٰ صُحُفٗا مُّنَشَّرَةٗ

Ati akufuna aliyense mwa iwo apatsidwe kalata zotambasulidwa (zimene zitsimikize uthenga wa Mneneri Muhammad{s.a.w}). info
التفاسير:

external-link copy
53 : 74

كَلَّاۖ بَل لَّا يَخَافُونَ ٱلۡأٓخِرَةَ

Sichoncho! Koma kuti iwo sakuopa tsiku lachimaliziro. info
التفاسير:

external-link copy
54 : 74

كَلَّآ إِنَّهُۥ تَذۡكِرَةٞ

Sichoncho! Ndithu ichi (Qur’an) ndichikumbutso (chokwanira). info
التفاسير:

external-link copy
55 : 74

فَمَن شَآءَ ذَكَرَهُۥ

Choncho amene wafuna achikumbukire (amene sakufuna ndizake)! info
التفاسير:

external-link copy
56 : 74

وَمَا يَذۡكُرُونَ إِلَّآ أَن يَشَآءَ ٱللَّهُۚ هُوَ أَهۡلُ ٱلتَّقۡوَىٰ وَأَهۡلُ ٱلۡمَغۡفِرَةِ

Ndipo sangakumbukire pokhapokha Allah atafuna. Iye ndiye Amene ali woyenera kumuopa, ndiponso ndiye Mwini kukhululukira (amene akumuopa). info
التفاسير: