د قرآن کریم د معناګانو ژباړه - چیچوایي ژباړه - خالد ابراهیم بتیالا

Al-Mulk

external-link copy
1 : 67

تَبَٰرَكَ ٱلَّذِي بِيَدِهِ ٱلۡمُلۡكُ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ

۞ Watukuka ndi kudalitsika (Allah) Amene m’manja Mwake muli ufumu (wochita chilichonse pazolengedwa zonse); ndipo Iye ali ndi mphamvu yokwanira pachilichonse.[370] info

[370] Sura imeneyi, Mtumiki (s.a.w) amafuna kuti msilamu aliyense ailoweze pamtima ndi kuzindikira bwino tanthauzo lake. Mtumiki (s.a.w) adali ndi chizolowezi chomawerenga Surayi asanagone. M’sura imeneyi muli chikumbutso chosonyeza kuti Allah Ngwamphamvu amachita mmene angafunire. Chimene wafuna chichitika ngakhale anthu sakufuna. Ndipo chimene sanafune kuti chichitike sichingachitike ngakhale anthu atafunitsitsa kuti chichitike. Zonse zakumwamba ndi zam’nthaka ndiZake.

التفاسير:

external-link copy
2 : 67

ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡمَوۡتَ وَٱلۡحَيَوٰةَ لِيَبۡلُوَكُمۡ أَيُّكُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلٗاۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفُورُ

Amene adalenga imfa ndi moyo kuti akuyeseni (mayeso) ndani mwa inu ali wochita zabwino (kwambiri). Ndipo Iye ndiWopambana m’mphamvu (salephera kanthu) ndiponso Wokhululukira (olakwa).[371] info

[371] M’ma Ayah awa:- Allah akutilangiza kuti tikhale oganizira zomwe adalenga zimene zingatisonyeze nzeru Zake ndi mphamvu Zake zakuya. Tilingalire m’zolengedwa Zake, tisalingalire mwa Iye mwini chifukwa sitingathe kumlingalira mmene alili pomwe tikulephera kuulingalira mzimu wathu momwe ulili.

التفاسير:

external-link copy
3 : 67

ٱلَّذِي خَلَقَ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖ طِبَاقٗاۖ مَّا تَرَىٰ فِي خَلۡقِ ٱلرَّحۡمَٰنِ مِن تَفَٰوُتٖۖ فَٱرۡجِعِ ٱلۡبَصَرَ هَلۡ تَرَىٰ مِن فُطُورٖ

Amene adalenga thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikana (kapena zolingana mkalengedwe kake). Suona kusiyana m’zolenga za Wachifundo chambiri. Bwereza kuyang’ana, kodi ukuona pena pong’ambika? info
التفاسير:

external-link copy
4 : 67

ثُمَّ ٱرۡجِعِ ٱلۡبَصَرَ كَرَّتَيۡنِ يَنقَلِبۡ إِلَيۡكَ ٱلۡبَصَرُ خَاسِئٗا وَهُوَ حَسِيرٞ

Bwerezanso kuyang’ana kachiwiri, kuyang’anako kukubwerera wekha (uku maso) ali olobodoka ndiponso otopa. (Suona polakwika paliponse). info
التفاسير:

external-link copy
5 : 67

وَلَقَدۡ زَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِمَصَٰبِيحَ وَجَعَلۡنَٰهَا رُجُومٗا لِّلشَّيَٰطِينِۖ وَأَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابَ ٱلسَّعِيرِ

Ndipo ndithu talikongoletsa thambo loyandikirali ndi nyali (nyenyezi) ndipo tazichita kukhala (mochokera zenje) zolasila asatana. Ndipo tawakonzera (patsiku lachimaliziro) chilango cha Moto woyaka. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 67

وَلِلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ

Ndipo kwa amene sakhulupirira Mbuye wawo ali nacho chilango cha Jahannam; ndipo kuipirenji kobwerera! info
التفاسير:

external-link copy
7 : 67

إِذَآ أُلۡقُواْ فِيهَا سَمِعُواْ لَهَا شَهِيقٗا وَهِيَ تَفُورُ

Akadzaponyedwa m’menemo adzamva mavume ake (oipa) uku ukuwira mwaukali. info
التفاسير:

external-link copy
8 : 67

تَكَادُ تَمَيَّزُ مِنَ ٱلۡغَيۡظِۖ كُلَّمَآ أُلۡقِيَ فِيهَا فَوۡجٞ سَأَلَهُمۡ خَزَنَتُهَآ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ نَذِيرٞ

Udzayandikira kudukaduka chifukwa cha mkwiyo (kukwiira oipa); nthawi iliyonse gulu (la oipa) likadzaponyedwa m’menemo, Angelo oyang’anira Motowo adzawafunsa (mowadzudzula): “Kodi sadakufikeni mchenjezi (wokuchenjezani za tsikuli?).” info
التفاسير:

external-link copy
9 : 67

قَالُواْ بَلَىٰ قَدۡ جَآءَنَا نَذِيرٞ فَكَذَّبۡنَا وَقُلۡنَا مَا نَزَّلَ ٱللَّهُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ كَبِيرٖ

Adzayankha “Inde, adatifika mchenjezi koma tidatsutsa, ndipo tidati: ‘Allah sadavumbulutse chilichonse (kwa iwe ngakhale kwa anzako). Koma inu muli m’kusokera kwakukulu.” info
التفاسير:

external-link copy
10 : 67

وَقَالُواْ لَوۡ كُنَّا نَسۡمَعُ أَوۡ نَعۡقِلُ مَا كُنَّا فِيٓ أَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ

Ndipo adzanena: “Tikadakhala kuti tidamvera (zimene ankatiuza) kapena kuziganizira mwanzeru sitikadakhala m’gulu la anthu a ku Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
11 : 67

فَٱعۡتَرَفُواْ بِذَنۢبِهِمۡ فَسُحۡقٗا لِّأَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ

Choncho adzavomereza machimo awo (koma sipadzakhala chopindula;) tero kuonongeka ndi kukhala kutali (ndi chifundo cha Allah) kuli pa anthu a ku Moto! info
التفاسير:

external-link copy
12 : 67

إِنَّ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٞ كَبِيرٞ

Ndithudi amene akumuopa Mbuye wawo pomwe iwo sakumuona, adzapeza chikhululuko pa machimo awo ndi malipiro aakulu (pa zabwino zomwe ankachita). info
التفاسير: