ߞߎ߬ߙߣߊ߬ ߞߟߊߒߞߋ ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߛ߭ߌߛ߭ߌߦߏߥߊߞߊ߲ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߞ߭ߊ߯ߟߌߘߎ߫ ߌߓߑߙߊ߬ߤߌ߯ߡߎ߫ ߔߌߕߊߟߊ߯

external-link copy
2 : 8

إِنَّمَا ٱلۡمُؤۡمِنُونَ ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِرَ ٱللَّهُ وَجِلَتۡ قُلُوبُهُمۡ وَإِذَا تُلِيَتۡ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُهُۥ زَادَتۡهُمۡ إِيمَٰنٗا وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ

Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa).[190] info

[190] Apa patchulidwa ena mwa makhalidwe a Asilamu omwe ngokwanira pachikhulupiliro chawo. Amene alibe makhalidwe otere, ndiye kuti chikhulupiliro chawo nchosakwanira ndipo pa tsiku la chimaliziro sichidzawapindulira zabwino.

التفاسير: