ߞߎ߬ߙߣߊ߬ ߞߟߊߒߞߋ ߞߘߐ ߟߎ߬ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߛ߭ߌߛ߭ߌߦߏߥߊߞߊ߲ ߘߟߊߡߌߘߊ - ߞ߭ߊ߯ߟߌߘߎ߫ ߌߓߑߙߊ߬ߤߌ߯ߡߎ߫ ߔߌߕߊߟߊ߯

external-link copy
135 : 6

قُلۡ يَٰقَوۡمِ ٱعۡمَلُواْ عَلَىٰ مَكَانَتِكُمۡ إِنِّي عَامِلٞۖ فَسَوۡفَ تَعۡلَمُونَ مَن تَكُونُ لَهُۥ عَٰقِبَةُ ٱلدَّارِۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ

Nena: “E inu anthu anga! Chitani zanu (zimene mufuna) momwe mungathere. Nanenso ndichita zanga. Choncho mudzaziwa kuti ndani mapeto ake adzakhale ndi malo abwino. Ndithudi, sangapambane anthu ochita zoipa.”[173] info

[173] Ayah iyi ikusonyeza kuti munthu wapatsidwa ufulu wochita kapena kusachita poopera kuti angadzanene kuti adakakamizidwa. Apa nzachidziwikire kuti amene wasankha chabwino adzapeza chabwino. Ndipo yemwe wasankha choipa adzapeza choipa.

التفاسير: