पवित्र कुरअानको अर्थको अनुवाद - चेवा अनुवाद : खालिद इब्राहीम बेतियाला ।

Al-Mursalât

external-link copy
1 : 77

وَٱلۡمُرۡسَلَٰتِ عُرۡفٗا

Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana. info
التفاسير:

external-link copy
2 : 77

فَٱلۡعَٰصِفَٰتِ عَصۡفٗا

Ndi mphepo yamkuntho ikamakuntha. info
التفاسير:

external-link copy
3 : 77

وَٱلنَّٰشِرَٰتِ نَشۡرٗا

Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula. info
التفاسير:

external-link copy
4 : 77

فَٱلۡفَٰرِقَٰتِ فَرۡقٗا

Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama; info
التفاسير:

external-link copy
5 : 77

فَٱلۡمُلۡقِيَٰتِ ذِكۡرًا

Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri. info
التفاسير:

external-link copy
6 : 77

عُذۡرًا أَوۡ نُذۡرًا

Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo; info
التفاسير:

external-link copy
7 : 77

إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَوَٰقِعٞ

Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko), info
التفاسير:

external-link copy
8 : 77

فَإِذَا ٱلنُّجُومُ طُمِسَتۡ

Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake). info
التفاسير:

external-link copy
9 : 77

وَإِذَا ٱلسَّمَآءُ فُرِجَتۡ

Ndiponso pamene thambo lidzang‘ambidwa. info
التفاسير:

external-link copy
10 : 77

وَإِذَا ٱلۡجِبَالُ نُسِفَتۡ

Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi). info
التفاسير:

external-link copy
11 : 77

وَإِذَا ٱلرُّسُلُ أُقِّتَتۡ

Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo). info
التفاسير:

external-link copy
12 : 77

لِأَيِّ يَوۡمٍ أُجِّلَتۡ

Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)? info
التفاسير:

external-link copy
13 : 77

لِيَوۡمِ ٱلۡفَصۡلِ

Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa). info
التفاسير:

external-link copy
14 : 77

وَمَآ أَدۡرَىٰكَ مَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِ

Nchiyani chingakudziwitse za tsiku la chiweruzirolo? info
التفاسير:

external-link copy
15 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير:

external-link copy
16 : 77

أَلَمۡ نُهۡلِكِ ٱلۡأَوَّلِينَ

Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)? info
التفاسير:

external-link copy
17 : 77

ثُمَّ نُتۡبِعُهُمُ ٱلۡأٓخِرِينَ

Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba), info
التفاسير:

external-link copy
18 : 77

كَذَٰلِكَ نَفۡعَلُ بِٱلۡمُجۡرِمِينَ

Chomwecho tiwachitiranso ochimwa. info
التفاسير:

external-link copy
19 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير:

external-link copy
20 : 77

أَلَمۡ نَخۡلُقكُّم مِّن مَّآءٖ مَّهِينٖ

Kodi sitidakulengeni kuchokera ku madzi onyozeka, (madzi ambewu ya munthu)? info
التفاسير:

external-link copy
21 : 77

فَجَعَلۡنَٰهُ فِي قَرَارٖ مَّكِينٍ

Kenako tidawaika pamalo okhazikika (kuti chilengedwe chake chikwanire pamenepo), info
التفاسير:

external-link copy
22 : 77

إِلَىٰ قَدَرٖ مَّعۡلُومٖ

Mpaka nyengo yodziwika (imene tidaipima kuti mwana abadwe). info
التفاسير:

external-link copy
23 : 77

فَقَدَرۡنَا فَنِعۡمَ ٱلۡقَٰدِرُونَ

Tidaipima nyengoyo; taonani kupima bwino Ife opima! info
التفاسير:

external-link copy
24 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير:

external-link copy
25 : 77

أَلَمۡ نَجۡعَلِ ٱلۡأَرۡضَ كِفَاتًا

Kodi sitidaichite nthaka kukhala yofungatira, info
التفاسير:

external-link copy
26 : 77

أَحۡيَآءٗ وَأَمۡوَٰتٗا

Amoyo ndi akufa? info
التفاسير:

external-link copy
27 : 77

وَجَعَلۡنَا فِيهَا رَوَٰسِيَ شَٰمِخَٰتٖ وَأَسۡقَيۡنَٰكُم مَّآءٗ فُرَاتٗا

Ndipo tidaika m’menemo mapiri ataliatali (olimbitsa nthaka), ndipo takumwetsani madzi okoma. info
التفاسير:

external-link copy
28 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa). info
التفاسير:

external-link copy
29 : 77

ٱنطَلِقُوٓاْ إِلَىٰ مَا كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ

(Kudzanenedwa kwa okana tsiku la chimaliziro:) Pitani kuzimene mudali kuzitsutsa zija. info
التفاسير:

external-link copy
30 : 77

ٱنطَلِقُوٓاْ إِلَىٰ ظِلّٖ ذِي ثَلَٰثِ شُعَبٖ

Pitani kumthunzi (wautsi wa ku Moto) wa nthambi zitatu, info
التفاسير:

external-link copy
31 : 77

لَّا ظَلِيلٖ وَلَا يُغۡنِي مِنَ ٱللَّهَبِ

Simthunzi (wamtendere) ndiponso siwotchinjiriza ku malawi a Moto.” info
التفاسير:

external-link copy
32 : 77

إِنَّهَا تَرۡمِي بِشَرَرٖ كَٱلۡقَصۡرِ

Ndithu motowo umaponya mphalikira (mbaliwali) zazikulu ngati nyumba, info
التفاسير:

external-link copy
33 : 77

كَأَنَّهُۥ جِمَٰلَتٞ صُفۡرٞ

Zonga ngati ngamira zachikasu. info
التفاسير:

external-link copy
34 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (zimenezi). info
التفاسير:

external-link copy
35 : 77

هَٰذَا يَوۡمُ لَا يَنطِقُونَ

Ili ndi tsiku lomwe sadzayankhula. info
التفاسير:

external-link copy
36 : 77

وَلَا يُؤۡذَنُ لَهُمۡ فَيَعۡتَذِرُونَ

Ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo. info
التفاسير:

external-link copy
37 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (za tsiku limenelo). info
التفاسير:

external-link copy
38 : 77

هَٰذَا يَوۡمُ ٱلۡفَصۡلِۖ جَمَعۡنَٰكُمۡ وَٱلۡأَوَّلِينَ

(Adzauzidwa kuti): Ili ndi tsiku loweruza (pakati pa abwino ndi oipa takusonkhanitsani inu (otsutsa Muhammad {s.a.w}), ndi akale (otsutsa aneneri akale). info
التفاسير:

external-link copy
39 : 77

فَإِن كَانَ لَكُمۡ كَيۡدٞ فَكِيدُونِ

Ngati muli ndi ndale (yodzipulumutsira ku chilango Changa) ndichiteni ndaleyo! info
التفاسير:

external-link copy
40 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo la Allah). info
التفاسير:

external-link copy
41 : 77

إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي ظِلَٰلٖ وَعُيُونٖ

Ndithu oopa (Allah tsiku limenelo) adzakhala mu mthunzi ndi mitsinje, info
التفاسير:

external-link copy
42 : 77

وَفَوَٰكِهَ مِمَّا يَشۡتَهُونَ

Ndipo adzakhala ndi zipatso zomwe azidzazifuna. info
التفاسير:

external-link copy
43 : 77

كُلُواْ وَٱشۡرَبُواْ هَنِيٓـَٔۢا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ

(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani, imwani mokondwa chifukwa cha zabwino zomwe mudali kuchita (mu moyo wa dziko lapansi). info
التفاسير:

external-link copy
44 : 77

إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُحۡسِنِينَ

Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino. info
التفاسير:

external-link copy
45 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah) info
التفاسير:

external-link copy
46 : 77

كُلُواْ وَتَمَتَّعُواْ قَلِيلًا إِنَّكُم مُّجۡرِمُونَ

Idyani, sangalalani pang’ono m’kanthawi kochepa; ndithu inu ndinu ochimwa (chifukwa chakumphatikiza Allah ndi zolengedwa). info
التفاسير:

external-link copy
47 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah). info
التفاسير:

external-link copy
48 : 77

وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ٱرۡكَعُواْ لَا يَرۡكَعُونَ

Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Weramani, (pembedzani Allah).” sawerengera. info
التفاسير:

external-link copy
49 : 77

وَيۡلٞ يَوۡمَئِذٖ لِّلۡمُكَذِّبِينَ

Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (malamulo a Allah). info
التفاسير:

external-link copy
50 : 77

فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَهُۥ يُؤۡمِنُونَ

Kodi ndi nkhani iti imene adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi (Qur’an)? info
التفاسير: